AGALATIYA 3 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Chilamulo sichingathe kupulumutsa; chititsogolera kutifikitsa kwa Khristu

1 Agal. 5.7 Agalatiya opusa inu, anakulodzani ndani, inu amene Yesu Khristu anaonetsedwa pamaso panu, wopachikidwa?

2Aef. 1.13Ichi chokha ndifuna kuphunzira kwa inu, Kodi munalandira Mzimuyo ndi ntchito za lamulo, kapena ndi kumva kwa chikhulupiriro?

3Agal. 4.9Kodi muli opusa otere? Popeza mudayamba ndi Mzimu, kodi tsopano mutsiriza ndi thupi?

42Yoh. 8Kodi mudamva zowawa zambiri zotere kwachabe? Ngatitu kwachabe.

5Ndipo iye amene akuonjezerani inu Mzimuyo, nachita zimphamvu mwa inu, atero kodi ndi ntchito za lamulo, kapena ndi kumva kwa chikhulupiriro?

6Gen. 15.6Monga Abrahamu anakhulupirira Mulungu, ndipo kunawerengedwa kwa iye chilungamo,

7Yoh. 8.39chotero zindikirani kuti iwo a chikhulupiriro ndiwo ana a Abrahamu.

8Gen. 18.18Ndipo malembo, pakuoneratu kuti Mulungu adzayesa olungama amitundu ndi chikhulupiriro, anayamba kale kulalikira Uthenga Wabwino kwa Abrahamu, kuti, Idzadalitsidwa mwa iwe mitundu yonse.

9Kotero kuti iwo a chikhulupiriro adalitsidwa pamodzi ndi Abrahamu wokhulupirikayo.

10Deut. 27.26; Yer. 11.3Pakuti onse amene atama ntchito za lamulo liwakhalira temberero; pakuti kwalembedwa,

Wotembereredwa aliyense

wosakhala m'zonse zolembedwa

m'buku la chilamulo, kuzichita izi.

11 Hab. 2.4; Agal. 2.16 Ndipo chidziwikatu kuti palibe munthu ayesedwa wolungama ndi lamulo pamaso pa Mulungu; pakuti, Wolungama adzakhala ndi moyo ndi chikhulupiriro;

12Lev. 18.5; Aro. 10.5koma chilamulo sichichokera kuchikhulupiriro; koma, Wakuzichita izi adzakhala ndi moyo ndi izi.

13Deut. 21.23; Aro. 8.3Khristu anatiombola ku temberero la chilamulo, atakhala temberero m'malo mwathu; pakuti kwalembedwa,

Wotembereredwa aliyense wopachikidwa pamtengo.

14 Zek. 12.10; Aro. 4.9, 16 Kuti dalitso la Abrahamu mwa Khristu Yesu, lichitike kwa amitundu; kuti tikalandire lonjezano la Mzimuyo, mwa chikhulupiriro.

15Abale, ndinena monga munthu. Pangano, lingakhale la munthu, litalunzika, palibe munthu aliyesa chabe, kapena kuonjezapo.

16Gen. 12.3, 7; Agal. 3.8Ndipo malonjezano ananenedwa kwa Abrahamu ndi kwa mbeu yake. Sanena, Ndipo kwa zimbeu, ngati kunena zambiri; komatu ngati kunena imodzi, Ndipo kwa mbeu yako, ndiye Khristu.

17Eks. 12.40-41; Aro. 4.13-14Ndipo ichi ndinena: Lamulo, limene linafika zitapita zaka mazana anai mphambu makumi atatu, silifafaniza pangano lolunzika kale ndi Mulungu, kuliyesa lonjezanolo lachabe.

18Aro. 4.13-14Pakuti ngati kulowa nyumba kuchokera kulamulo, sikuchokeranso kulonjezano; koma kumeneku Mulungu anampatsa Abrahamu kwaufulu mwa lonjezano.

19Yoh. 1.17; Aro. 5.20; Agal. 3.16Nanga chilamulo tsono? Chinaonjezeka chifukwa cha zolakwa, kufikira ikadza mbeu imene adailonjezera; ndipo chinakonzeka ndi angelo m'dzanja la nkhoswe.

20Koma nkhoswe siili ya mmodzi; koma Mulungu ali mmodzi.

21Agal. 2.21Pamenepo kodi chilamulo chitsutsana nao malonjezano a Mulungu? Msatero ai. Pakuti chikadapatsidwa chilamulo chakukhoza kuchitira moyo, chilungamo chikadachokera ndithu kulamulo.

22Aro. 3.9, 19, 23; 4.11-12, 16Komatu lembo linatsekereza zonse pansi pa uchimo, kuti lonjezano la kwa chikhulupiriro cha Yesu Khristu likapatsidwe kwa okhulupirirawo.

23Koma chisanadze chikhulupiriro tinasungidwa pomvera lamulo otsekedwa kufikira chikhulupiriro chimene chikavumbulutsidwa bwinobwino.

24Mat. 5.17; Mac. 13.49Momwemo chilamulo chidakhala namkungwi wathu wakutifikitsa kwa Khristu, kuti tikayesedwe olungama ndi chikhulupiriro.

25Koma popeza chadza chikhulupiriro, sitikhalanso omvera namkungwi.

261Yoh. 3.1-2Pakuti inu nonse muli ana a Mulungu, mwa chikhulupiriro cha mwa Khristu Yesu.

27Aro. 6.3Pakuti nonse amene munabatizidwa kwa Khristu mudavala Khristu.

28Yoh. 10.16; Aro. 10.12Muno mulibe Myuda, kapena Mgriki, muno mulibe kapolo, kapena mfulu, muno mulibe mwamuna ndi mkazi; pakuti muli nonse mmodzi mwa Khristu Yesu.

29Aro. 8.17Koma ngati muli a Khristu, muli mbeu ya Abrahamu, nyumba monga mwa lonjezano.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help