MASALIMO 82 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Oweruza aweruza bwinoSalimo la Asafu.

1Mulungu aima mu msonkhano wa Mulungu,

aweruza pakati pa milungu.

2 Deut. 1.17; Miy. 18.5 Mudzaweruza mosalunjika kufikira liti,

ndi kusamalira nkhope ya oipa?

3 Yer. 22.3 Weruzani osauka ndi amasiye;

weruzani molungama ozunzika ndi osowa.

4Pulumutsani osauka ndi aumphawi;

alanditseni m'dzanja la oipa.

5 Mik. 3.1-2 Sadziwa, ndipo sazindikira;

amayendayenda mumdima;

maziko onse a dziko lapansi agwedezeka.

6 Yoh. 10.34 Ndinati Ine, Inu ndinu milungu,

ndi ana a Wam'mwambamwamba nonsenu.

7Komatu mudzafa monga anthu,

ndipo mudzagwa monga wina wa akulu.

8 Mas. 2.8 Ukani, Mulungu, weruzani dziko lapansi;

pakuti Inu mudzalandira amitundu onse.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help