1Pamenepo Bilidadi wa ku Suki anayankha, nati,
2Musaka mau kufikira liti?
Zindikirani, ndi pamenepo tidzanena.
3Tiyesedwa bwanji ngati nyama zakuthengo,
ndi kukhala odetsedwa pamaso panu?
4Iwe wodzing'amba mumkwiyo mwako,
kodi dziko lapansi lisiyidwe chifukwa cha iwe?
Kapena thanthwe lisunthike m'malo mwake?
5 Miy. 13.9 Inde, kuunika kwa woipa kudzazima,
ndi lawi la moto wake silidzawala.
6Kuunikaku kudzada m'hema mwake,
ndi nyali yake ya pamwamba pake idzazima.
7Mapondedwe ake amphamvu adzasautsidwa,
ndi uphungu wakewake udzamgwetsa.
8 Mas. 35.8 Pakuti aponyedwa mu ukonde ndi mapazi ake,
namaponda pamatanda.
9Msampha udzamgwira kuchitendeni,
ndi khwekhwe lidzamkola.
10Msampha woponda umbisikira pansi,
ndi msampha wa chipeto panjira.
11 Yer. 6.25 Zoopetsa zidzamchititsa mantha monsemo,
nadzampirikitsa kumbuyo kwake.
12Njala idzatha mphamvu yake,
ndi tsoka lidzamkonzekeratu pambali pake.
13Zidzatha ziwalo za thupi lake,
mwana woyamba wa imfa adzatha ziwalo zake.
14 Miy. 10.28 Adzazulidwa kuhema kwake kumene anakhulupirira;
nadzatengedwa kunka naye kwa mfumu ya zoopsa.
15Adzakhala m'hema mwake iwo amene sali ake;
miyala ya sulufure idzawazika pokhala pake.
16 Yes. 5.24 Mizu yake idzauma pansi,
ndi nthambi yake idzafota m'mwamba.
17 Mas. 34.16 Chikumbukiro chake chidzatayika m'dziko,
ndipo adzasowa dzina kukhwalala.
18Adzamkankha achoke kukuunika alowe kumdima;
adzampirikitsa achoke m'dziko lokhalamo anthu.
19Sadzakhala naye mwana kapena chidzukulu
mwa anthu a mtundu wake,
kapena wina wotsalira kumene anakhalako.
20Akudza m'mbuyo adzadabwa nalo tsiku lake,
monga aja omtsogolera anagwidwa mantha.
21 Yer. 9.3; 1Ate. 4.5; 2Ate. 1.8; Tit. 1.16 Zoonadi, zokhalamo osalungama zitero,
ndi malo a iye amene sadziwa Mulungu ndi awa.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.