1 MBIRI 22 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Davide akonzeratu mirimo yakumanga Kachisi

1 2Mbi. 3.1 Ndipo Davide anati, Pano padzakhala nyumba ya Yehova Mulungu, ndi pano padzakhala guwa la nsembe yopsereza la Israele.

2Ndipo Davide anati asonkhanitse alendo okhala m'dziko la Israele; iye naika osema miyala afukule miyala, aiseme kuti amange nayo nyumba ya Mulungu.

31Maf. 7.47; 1Mbi. 22.14Nakonzeratu Davide chitsulo chochuluka cha misomali ya ku zitseko za zipata, ndi ya kuphatikizitsa; ndi mkuwa wochuluka wosauyesa kulemera kwake;

41Maf. 5.6ndi mitengo yamikungudza yosaiwerenga; pakuti Asidoni ndi Atiro anabwera nayo kwa Davide mitengo yamikungudza yochuluka.

51Mbi. 29.1Ndipo Davide anati, Solomoni mwana wanga ndiye mnyamata ndi wosakhwima, ndi nyumba imene adzaimangira Yehova ikhale yaikulu yopambana, yomveka ndi ya ulemerero mwa maiko onse; ndiikonzeretu mirimo. Momwemo Davide anakonzeratu mochuluka asanamwalire.

Davide amlangiza Solomoni ammangire Yehova nyumba

6Pamenepo iye anaitana Solomoni mwana wake, namlangiza ammangire Yehova Mulungu wa Israele nyumba.

71Maf. 8.17Ndipo Davide anati kwa Solomoni mwana wake, Kunena za ine, kumtima kwanga kudati, ndilimangire dzina la Yehova Mulungu wanga nyumba.

81Maf. 5.3-5Koma mau a Yehova anandidzera, kuti, Wakhetsa mwazi wochuluka, popeza wachita nkhondo zazikulu; sudzamangira dzina langa nyumba, popeza wakhetsa pansi mwazi wambiri pamaso panga;

9taona, udzabala mwana, ndiye adzakhala munthu wa phee; ndipo ndidzampumulitsira adani ake onse pozungulirapo, pakuti dzina lake lidzakhala Solomoni; ndipo ndidzapatsa Israele mtendere ndi bata masiku ake;

10iyeyu adzamangira dzina langa nyumba; iye adzakhala mwana wanga, ndi Ine ndidzakhala Atate wake; ndipo ndidzakhazikitsa mpando wachifumu wa ufumu wake pa Israele, kosalekeza.

11Tsono, mwana wanga, Yehova akhale nawe; nulemerere, numange nyumba ya Yehova Mulungu wako monga ananena za iwe.

121Maf. 3.9, 12Chokhachi, Yehova akupatse nzeru ndi luntha, nakulangize za Israele, kuti usunge chilamulo cha Yehova Mulungu wako.

13Yos. 1.6-9Momwemo udzalemerera, ukasamalira kuchita malemba ndi maweruzo amene Yehova analangiza Mose za Israele; limbikatu, nulimbike mtima, usaope, usade mtima.

141Mbi. 22.3Taona tsono, m'kuzunzika kwanga ndinakonzeratu nyumba ya Yehova matalente zikwi zana limodzi a golide, ndi matalente zikwizikwi a siliva, ndi mkuwa, ndi chitsulo, osayesa kulemera kwake, pakuti zidachulukadi; mitengo yomwe ndi miyala ndakonzeratu; nuonjezereko.

15Uli naonso antchito ochuluka ofukula miyala, ndi amisiri a miyala ndi a mitengo, ndi amuna onse aluso akuchita ntchito zilizonse;

16golide, ndi siliva, ndi mkuwa, ndi chitsulo, nzosawerengeka; nyamuka, nuchite, Yehova akhale nawe.

17Davide analangizanso akalonga a Israele athandize Solomoni mwana wake, ndi kuti,

18Deut. 12.10; 2Sam. 7.1Kodi Yehova Mulungu wanu sali nanu? Sanakupumulitseni pambali ponse? Pakuti anapereka nzika za m'dziko m'dzanja mwanga, ndi dziko lagonjetsedwa pamaso pa Yehova, ndi pamaso pa anthu ake.

19Deut. 4.29; 1Maf. 8.6, 21; 1Mbi. 22.7Perekani tsono mtima ndi moyo wanu kufunafuna Yehova Mulungu wanu; ndipo nyamukani ndi kumanga malo opatulika a Yehova Mulungu, kuti abwere nalo likasa la chipangano la Yehova, ndi zipangizo zopatulika za Mulungu, kunyumba imene idzamangidwira dzina la Yehova.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help