EZARA 5 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Zerubabele ndi Yesuwa apitirira kumanga Kachisi

1 Hag. 1.1; Zek. 1.1 Ndipo aneneri, Hagai mneneriyo, ndi Zekariya mwana wa Ido, ananenera kwa Ayuda okhala mu Yuda ndi mu Yerusalemu; m'dzina la Mulungu wa Israele ananenera kwa iwo.

2Pamenepo Zerubabele mwana wa Sealatiele, ndi Yesuwa mwana wa Yozadaki, ananyamuka, nayamba kumanga nyumba ya Mulungu ili ku Yerusalemu, anali pamodzi nao aneneri a Mulungu akuwathandiza.

3Nthawi yomweyi anawadzera Tatenai kazembe tsidya lino la mtsinjewo, ndi Setari-Bozenai, ndi anzao, nanena nao motere, Anakulamulirani inu ndani kumanga nyumba iyi, ndi kutsiriza khoma ili?

4Nanena naonso motere, Maina ao a anthu omanga chimangidwe ichi ndiwo ayani?

5Ezr. 7.6, 28; Mas. 33.18Koma diso la Mulungu wao linali pa akulu a Ayuda, ndipo sanawaletse mpaka mlandu unamdzera Dariusi, nabweza mau a mlanduwo m'kalata.

Tatenai awaneneza kwa Dariusi

6Zolembedwa m'kalata amene Tatenai kazembe wa tsidya lino la mtsinjewo, ndi Setari-Bozenai, ndi anzake Afarisikai, okhala tsidya lino la mtsinje, anatumiza kwa Dariusi mfumu,

7anatumiza kalata kwa iyeyo m'menemo munalembedwa motere, kwa Dariusi mfumu, mtendere wonse.

8Adziwe mfumu kuti ife tinamuka kudziko la Yuda, kunyumba ya Mulungu wamkulu, yomangidwa ndi miyala yaikulu, ndi kuikidwa mitengo pamakoma, ndipo inachitika mofulumira ntchitoyi, ndipo inayenda bwino m'dzanja mwao.

9Ezr. 5.3-4Pamenepo tinafunsa akulu aja ndi kutere nao, Anakulamulirani ndani kumanga nyumba iyi, ndi kutsiriza khoma ili?

10Tinawafunsanso maina ao, kukudziwitsani, kuti tilembere maina a anthu akuwatsogolera.

111Maf. 6.1Natiyankha mau motere, ndi kuti, Ife ndife akapolo a Mulungu wa kumwamba ndi dziko lapansi, tilikumanga nyumba imene idamangika zapita zaka zambiri; inaimanga ndi kuitsiriza mfumu yaikulu ya Israele.

122Maf. 24.1-2Koma makolo athuwo atautsa mkwiyo wa Mulungu wa Kumwamba, Iye anawapereka m'dzanja la Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni Mkaldeya, amene anaononga nyumba ino, natenga anthu ndende kunka nao ku Babiloni.

13Koma chaka choyamba cha Kirusi mfumu ya Babiloni, Kirusi mfumuyo analamulira kuti azimanga nyumba iyi ya Mulungu.

14Ezr. 1.7-8; Hag. 2.2, 21Ndiponso zipangizo za golide ndi siliva za nyumba ya Mulungu, anazitulutsa Nebukadinezara mu Kachisi anali ku Yerusalemu, ndi kubwera nazo ku Kachisi wa ku Babiloni, izizo Kirusi mfumu anazitulutsa mu Kachisi wa ku Babiloni, nazipereka kwa munthu dzina lake Sezibazara, amene anamuika akhale kazembe;

15nati naye, Tenga zipangizo izi, kaziike mu Kachisi ali mu Yerusalemu, nimangidwe nyumba ya Mulungu pambuto pake.

16Ezr. 3.8, 10Pamenepo anadza Sezibazara yemweyo namanga maziko a nyumba ya Mulungu ili mu Yerusalemu; ndipo kuyambira pomwepo kufikira tsopano ilinkumangidwa, koma siinatsirizike.

17Ndipo tsono chikakomera mfumu, munthu asanthule m'nyumba ya chuma cha mfumu ili komwe ku Babiloni, ngati nkuterodi, kuti Kirusi mfumu analamulira kuti azimanga nyumba iyi ya Mulungu ku Yerusalemu; ndipo mfumu ititumizire mau omkomera pa chinthuchi.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help