MASALIMO 48 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Ukoma ndi ulemerero wa ZiyoniNyimbo. Salimo la ana a Kora.

1 Yes. 2.2-3 Yehova ndiye wamkulu, ayenera kulemekezekadi,

m'mzinda wa Mulungu wathu, m'phiri lake loyera.

2 Mas. 50.2; Ezk. 20.6; Mat. 5.35 Phiri la Ziyoni, chikhalidwe chake nchokoma

kumbali zake za kumpoto,

ndilo chimwemwe cha dziko lonse lapansi,

mzinda wa mfumu yaikulu.

3Mulungu adziwika m'zinyumba zake ngati msanje.

4 2Sam. 10.6-19 Pakuti, taonani, mafumuwo anasonkhana,

anapitira pamodzi.

5Anapenya mudziwo, ndipo pamenepo anadabwa;

anaopsedwa, nathawako.

6Pomwepo anagwidwa nako kunthunthumira;

anamva chowawa, ngati wam'chikuta.

7 Ezk. 27.25-26 Muswa zombo za ku Tarisisi ndi mphepo ya kum'mawa.

8Monga tidamva, momwemo tidapenya

m'mzinda wa Yehova wa makamu, m'mzinda wa Mulungu wathu,

Mulungu adzaukhazikitsa kunthawi yamuyaya.

9 Mas. 40.10 Tidalingalira zachifundo chanu, Mulungu,

m'kati mwa Kachisi wanu.

10 Deut. 28.58 Monga dzina lanu, Mulungu,

momwemo lemekezo lanu ku malekezero a dziko lapansi;

m'dzanja lamanja lanu mudzala chilungamo.

11Likondwere phiri la Ziyoni,

asekere ana aakazi a Yuda,

chifukwa cha maweruzo anu.

12Zungulirani Ziyoni, ndipo muuzinge,

werengani nsanja zake.

13 Mas. 56.13; Hos. 13.14 Penyetsetsani malinga ake,

yesetsani zinyumba zake;

kuti mukaziwerengere mibadwo ikudza m'mbuyo.

14 Yes. 58.11 Pakuti Mulungu ameneyo ndiye Mulungu wathu

kunthawi za nthawi,

adzatitsogolera kufikira imfa.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help