YOBU 2 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

1 Yob. 1.6-8 Panalinso tsiku lakuti anadza ana a Mulungu kudzionetsa kwa Yehova, nadza Satana yemwe pakati pao kudzionetsa kwa Yehova.

2Ndipo Yehova anati kwa Satana, Ufuma kuti? Nayankha Satana, nati kwa Yehova, Kupitapita m'dziko, ndi kuyendayenda m'mwemo.

3Ndipo Yehova anati kwa Satana, Kodi waonerera mtumiki wanga Yobu? Pakuti palibe wina wonga iye m'dzikomo, munthu wangwiro ndi woongoka, wakuopa Mulungu, ndi kupewa zoipa; naumirirabe kukhala wangwiro, chinkana undisonkhezera ndimuononge kopanda chifukwa.

4Nayankha Satana, nati kwa Yehova, Khungu kulipa khungu, inde munthu adzapereka zonse ali nazo kuombola moyo wake.

5Yob. 1.11Koma tambasulani dzanja lanu, ndi kukhudza fupa lake ndi mnofu wake, ndipo adzakuchitirani mwano pamaso panu.

6Ndipo Yehova anati kwa Satana, Taona, akhale m'dzanja lako; moyo wake wokha uuleke.

7Natuluka Satana pamaso pa Yehova, nazunza Yobu ndi zilonda zowawa, kuyambira kuphazi lake kufikira pakati pamutu pake.

8Ndipo anadzitengera phale, kudzikanda nalo; nakhala pansi m'maphulusa.

9Pamenepo mkazi wake ananena naye, Kodi uumiriranso kukhala wangwiro? Chitira Mulungu mwano, ufe.

10Yob. 1.22; Mas. 39.1; Aro. 12.12; Yak. 5.10-11Koma ananena naye, Ulankhula monga amalankhula akazi opusa. Ha! Tidzalandira zokoma kwa Mulungu kodi, osalandiranso zoipa? Pa ichi chonse Yobu sanachimwe ndi milomo yake.

Mabwenzi ake atatu adzacheza naye

11 Miy. 17.17; Aro. 12.15 Atamva tsono mabwenzi atatu a Yobu za choipa ichi chonse chidamgwera, anadza, yense kuchokera kwao, Elifazi wa ku Temani, ndi Bilidadi Msuki, ndi Zofari wa ku Naama, napangana kudzafika kumlirira ndi kumsangalatsa.

12Ezk. 27.30Ndipo pokweza maso ao ali kutali, sanamdziwe, nakweza mau ao, nalira; nang'amba yense malaya ake, nawaza fumbi kumwamba ligwe pamitu pao.

13Gen. 50.10; Ezk. 3.14, 16Nakhala pansi pamodzi naye panthaka masiku asanu ndi awiri usana ndi usiku, palibe mmodzi ananena naye kanthu, popeza anaona kuti kuwawaku nkwakukulu ndithu.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help