2 ATESALONIKA Mau Oyamba - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu
Mau OyambaNgakhale Paulo awalembera kalata ija, Atesalonika adakhala akutsutsanabe pa za kubweranso kwa Ambuye, mwakuti panali chisokonezo. Ena mwa iwo ankati tsiku la kubwera kwa Khristu lafika kale. Tsono Paulo awalembera kalata yachiwiri, kuwadziwitsa kuti Khristu asanabwere, zinthu zidzaipiratu, pakuti padzafika wina wake wotchedwa “Woipitsitsa uja” amene adzalimbane ndi Khristu, mwakuti zoipa zija zidzafika pake penipeni.Nchifukwa chake Paulo akuwauza Akhristu kuti asaope zovuta ndi mazunzo, koma akhale ndi chikhulupiriro cholimba, abagwira ntchito kuti apeze chakudya, monga momwe iye ndi anzake amachitira, ndipo apitirize kuchita zabwino.Za mkatimuMau oyamba 1.1-2Ayamikira chikhulupiriro chao ndipo awachenjeza 1.3-13Za kubwera kwa Woipitsitsa uja 2.1-17Malangizo okhudza moyo wao wa Chikhristu 3.1-15Mau omaliza 3.16-18