YESAYA 60 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Ulemerero wa Yerusalemu ubwezedwa

1 Aef. 5.14; Mala. 4.2 Nyamuka, wala, pakuti kuunika kwako kwafika, ndi ulemerero wa Yehova wakutulukira.

2Pakuti taona, mdima udzaphimba dziko lapansi, ndi mdima wa bii mitundu ya anthu; koma Yehova adzakutulukira ndi ulemerero wake udzaoneka pa iwe.

3Yes. 49.6, 23; Chiv. 21.24Ndipo amitundu adzafika kwa kuunika kwako, ndi mafumu kwa kuyera kwa kutuluka kwako.

4Yes. 49.18Tukula maso ako uunguzeunguze ndi kuona; iwo onse asonkhana pamodzi, adza kwa iwe; ana ako aamuna adzachokera kutali, ndi ana ako aakazi adzaleredwa pambali.

5Aro. 11.25Pamenepo udzaona ndi kuunikidwa, ndipo mtima wako udzanthunthumira ndi kukuzidwa; pakuti unyinji wa nyanja udzakutembenukira, chuma cha amitundu chidzafika kwa iwe.

6Gen. 25.4; Mas. 72.10; Mat. 2.11Gulu la ngamira lidzakukuta, ngamira zazing'ono za Midiyani ndi Efa; iwo onsewo adzachokera ku Sheba adzabwera nazo golide ndi lubani; ndipo adzalalikira matamando a Yehova.

7Gen. 25.13; Hag. 2.7, 9Zoweta za Kedara zidzasonkhana kwa iwe, nkhosa zamphongo za Nebayoti zidzakutumikira; izo zidzafika ndi kulandiridwa paguwa langa la nsembe; ndipo ndidzakometsa nyumba ya ulemerero wanga.

8Hos. 11.11Ndani awa amene auluka ngati mtambo, ndi monga nkhunda kumazenera ao?

9Mas. 72.10Zoonadi, zisumbu zidzandilindira Ine; zidzayamba ndi ngalawa za Tarisisi kutenga ana ako aamuna kutali, golide wao ndi siliva wao pamodzi nao, chifukwa cha dzina la Yehova Mulungu wako, ndi chifukwa cha Woyera wa Israele, popeza Iye wakukometsa iwe.

10Yes. 54.7-8; Zek. 6.15Ndipo alendo adzamanga malinga ako, ndi mafumu ao adzakutumikira; pakuti m'kukwiya kwanga ndinakantha, koma mokomera mtima ndidakuchitira iwe chifundo.

11Chiv. 21.25Zipata zako zidzakhalabe zotseguka, sizidzatsekedwa usana pena usiku, kuti abwere nacho kwa iwe chuma cha amitundu, ndi mafumu ao otsogozedwa nao pamodzi.

12Mat. 21.44Pakuti mtundu ndi ufumu umene udzakana kukutumikira udzaonongeka; inde mitundu imeneyo idzasakazidwa ndithu.

131Mbi. 28.1-2; Yes. 35.2Ulemerero wa Lebanoni udzafika kwa iwe; mtengo wamlombwa, mtengo wamkuyu ndi mtengo wanaphini pamodzi, kukometsera malo a Kachisi wanga; ndipo ndidzachititsa malo a mapazi anga ulemerero.

14Yes. 49.23Ndipo ana aamuna a iwo amene anavuta iwe adzafika, nadzakugwadira; ndipo iwo onse amene anakuchepetsa iwe adzagwadira kumapazi ako, nadzakutcha iwe, Mzinda wa Yehova, Ziyoni wa Woyera wa Israele.

15Ungakhale unasiyidwa ndi kudedwa, osapita munthu mwa iwe, Ine ndidzakusandutsa changwiro chosatha, chokondweretsa cha mibadwo yambiri.

16Yes. 43.3; 49.26Iwe udzayamwanso mkaka wa amitundu, nudzayamwa bere la mafumu, nudzadziwa kuti Ine Yehova ndine Mpulumutsi wako, ndi Mombolo wako, Wamphamvu ya Yakobo.

17M'malo mwa mkuwa ndidzatenga golide, ndi m'malo mwa chitsulo ndidzatenga siliva, ndi m'malo mwa mtengo ndidzatenga mkuwa, ndi m'malo mwa miyala ndidzatenga chitsulo; ndidzakuikira akapitao a mtendere, ndi oyang'anira ntchito a chilungamo.

18Yes. 26.1Chiwawa sichidzamvekanso m'dziko mwako, kupululutsa pena kupasula m'malire ako; koma udzatcha malinga ako Chipulumutso, ndi zipata zako Matamando.

19Chiv. 21.23; 22.5Dzuwa silidzakhalanso kuunika kwako usana, ngakhale mwezi sudzakuunikiranso kuti kuyere; koma Yehova adzakhala kwa iwe kuunika kosatha, ndi Mulungu wako adzakhala ulemerero wako.

20Chiv. 21.23; 22.5Dzuwa lako silidzalowanso, mwezi wako sudzanka kumidima; pakuti Yehova adzakhala kuunika kwako kosatha, ndi masiku a kulira maliro ako adzatha.

21Mas. 37.11, 22Anthu ako adzakhalanso onse olungama; dzikolo lidzakhala cholowa chao kunthawi zonse, nthambi yooka Ine, ntchito ya manja anga, kuti Ine ndikuzidwe.

22Yes. 61.3; Mat. 13.31-32Wamng'ono adzasanduka chikwi, ndi wochepa adzasanduka mtundu wamphamvu; Ine Yehova ndidzafulumiza ichi m'nthawi yake.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help