MASALIMO 101 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Davide akuti adzasamala okhulupirika nadzachotsa oipaSalimo la Davide.

1 Mas. 89.1 Ndidzaimba zachifundo ndi chiweruzo;

ndidzaimba zakukulemekezani Inu, Yehova.

2 1Maf. 9.4 Ndidzachita mwanzeru m'njira yangwiro;

mudzandidzera liti?

Ndidzayenda m'nyumba mwanu ndi mtima wangwiro.

3 Mas. 97.10 Sindidzaika chinthu choipa pamaso panga;

chochita iwo akupatuka padera chindiipira;

sichidzandimamatira.

4Mtima wopulukira udzandichokera;

sindidzadziwana naye woipa.

5 Mas. 15.3; Miy. 6.17 Wakuneneza mnzake m'tseri ndidzamdula;

wa maso odzikuza ndi mtima wodzitama sindidzamlola.

6Maso anga ayang'ana okhulupirika m'dziko, kuti akhale ndi Ine;

iye amene ayenda m'njira yangwiro, iyeyu adzanditumikira Ine.

7 Mas. 120.2 Wakuchita chinyengo sadzakhala m'kati mwa nyumba yanga;

wakunena mabodza sadzakhazikika pamaso panga.

8 Yer. 21.12 Mamawa onse ndidzadula oipa onse a m'dziko;

kuduliratu onse akuchita zopanda pake kumzinda wa Yehova.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help