1 Yes. 26.9 Usiku pamphasa panga ndinamfunafuna amene moyo wanga umkonda:
Ndinamfunafuna, koma osampeza.
2Ndinati, Ndiuketu, ndiyendeyende m'mzinda,
m'makwalala ndi m'mabwalo ake,
ndimfunefune amene moyo wanga umkonda:
Ndimfunafuna, koma osampeza.
3Alonda akuyendayenda m'mzinda anandipeza:
Ndinati, Kodi munamuona amene moyo wanga umkonda?
4Nditawapitirira pang'ono,
ndinampeza amene moyo wanga umkonda:
Ndinamgwiritsitsa, osamfumbatula,
mpaka nditamlowetsa m'nyumba ya amai,
ngakhale m'chipinda cha wondibala.
5Ndikulumbirirani, ana aakazi inu a ku Yerusalemu,
pali mphoyo, ndi mbawala yakuthengo,
kuti musautse, ngakhale kugalamutsa chikondi,
mpaka chikafuna mwini.
Ulendo wa ukwati6 Yes. 60.8 Ndaniyu akwera kutuluka m'chipululu ngati utsi wa tolo,
wonunkhira ndi mure ndi lubani,
ndi zonunkhiritsa zonse za wogulitsa?
7Taonani, ndi machira a Solomoni;
pazingapo amuna amphamvu makumi asanu ndi limodzi,
a mwa ngwazi za Israele.
8Onsewo agwira lupanga, nazolowera nkhondo:
Yense ali ndi lupanga lake pantchafu pake,
chifukwa cha upandu wa usiku.
9Solomoni mfumu anadzipangira machira okhalamo tsonga
ndi matabwa a ku Lebanoni.
10Anapanga timilongoti take ndi siliva,
cha pansi pake ndi golide, mpando wake ndi nsalu yofiirira,
pakati pake panayalidwa za chikondi
cha ana aakazi a ku Yerusalemu.
11Tulukani, ana aakazi inu a Ziyoni,
mupenye Solomoni mfumu,
ndi korona amake amamveka naye tsiku la ukwati wake,
ngakhale tsiku lakukondwera mtima wake.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.