AEFESO 3 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Chinsinsi cha maitanidwe a amitundu

1 Mac. 21.33 Chifukwa cha ichi ine Paulo, ndine wandende wa Khristu Yesu chifukwa cha inu amitundu,

2Mac. 9.15ngatitu munamva za udindo wa chisomo cha Mulungu chimene anandipatsa ine cha kwa inu;

3Agal. 1.12; Akol. 1.26-27ndi umo anandizindikiritsa chinsinsicho mwa vumbulutso, monga ndinalemba kale mwachidule,

4chimene mukhoza kuzindikira nacho, pakuchiwerenga, chidziwitso changa m'chinsinsi cha Khristu,

5Aef. 3.9; Aro. 16.25chimene sanachizindikiritse ana a anthu m'mibadwo ina, monga anachivumbulutsa tsopano kwa atumwi ndi aneneri ake oyera mwa Mzimu,

6Agal. 3.28-29kuti amitundu ali olowa nyumba pamodzi ndi ife, ndi ziwalo zinzathu za thupilo, ndi olandira nafe pamodzi palonjezano mwa Khristu Yesu, mwa Uthenga Wabwino,

7Akol. 1.23, 25umene anandikhalitsa mtumiki wake monga mwa mphatso ya chisomo cha Mulungu, chimene anandipatsa ine, monga mwa machitidwe a mphamvu yake.

81Ako. 15.9Kwa ine wochepa ndi wochepetsa wa onse oyera mtima anandipatsa chisomo ichi ndilalikire kwa amitundu chuma chosalondoleka cha Khristu;

9Aef. 3.3ndi kuwalitsira onse adziwe makonzedwe a chinsinsicho, chimene chinabisika kuyambira kalekale mwa Mulungu wolenga zonse;

101Tim. 3.16kuti mu Mpingo azindikiritse tsopano kwa akulu ndi maulamuliro m'zakumwamba nzeru ya mitundumitundu ya Mulungu,

11Yoh. 6.33, 62monga mwa chitsimikizo mtima cha nthawi za nthawi, chimene anachita mwa Khristu Yesu Ambuye wathu:

12amene tili naye chokhazikika mtima ndi chiyandiko cholimbika, mwa chikhulupiriro cha pa Iye.

13Aef. 3.1Mwa ichi ndipempha kuti musade mtima m'zisautso zanga chifukwa cha inu, ndiwo ulemerero wanu.

Paulo apempherera Aefeso

14Chifukwa cha ichi ndipinda maondo anga kwa Atate,

15Afi. 2.9-11amene kuchokera kwa Iye fuko lonse la m'mwamba ndi la padziko alitcha dzina,

16Akol. 1.11kuti monga mwa chuma cha ulemerero wake akulimbikitseni inu ndi mphamvu mwa Mzimu wake, m'kati mwanu,

17Yoh. 14.23kuti Khristu akhale chikhalire mwa chikhulupiriro m'mitima yanu; kuti, ozika mizu ndi otsendereka m'chikondi,

18Aef. 1.18mukakhozetu kuzindikira pamodzi ndi oyera mtima onse, kupingasa, ndi utali, ndi kukwera,

19Akol. 2.9-10ndi kuzama nchiyani; ndi kuzindikira chikondi cha Khristu, chakuposa mazindikiridwe, kuti mukadzazidwe kufikira chidzalo chonse cha Mulungu.

20 Aro. 16.25 Ndipo kwa Iye amene angathe kuchita koposaposatu zonse zimene tizipempha, kapena tiziganiza, monga mwa mphamvu ya kuchita mwa ife,

21Aro. 11.36kwa Iye ukhale ulemerero mu Mpingo ndi mwa Khristu Yesu, kufikira mibadwo yonse ya nthawi za nthawi. Amen.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help