1Chaka chakhumi, mwezi wakhumi, tsiku lakhumi ndi chiwiri la mweziwo, anandidzera mau a Yehova, akuti,
2Yes. 19.1Wobadwa ndi munthu iwe, lozetsa nkhope yako itsutsane naye Farao mfumu ya Aejipito, nunenere motsutsana ndi iye, ndi Ejipito yense;
3Yer. 44.30nena, uziti, Atero Ambuye Yehova, Taona nditsutsana nawe, Farao mfumu ya Aejipito, ng'ona yaikulu yakugona m'kati mwa mitsinje yake, imene ikuti, Mtsinje wanga ndi wangatu, ndadzipangira ndekha uwu.
4Yes. 37.29Koma ndidzaika mbedza m'kamwa mwako, ndi kumamatiritsa nsomba za m'mitsinje mwako kumamba ako; ndipo ndidzakukweza kukutulutsa m'kati mwa mitsinje yako, pamodzi ndi nsomba zonse za m'mitsinje mwako zomamatira pa mamba ako.
5Yer. 7.33Ndipo ndidzakutaya kuchipululu, iwe ndi nsomba zonse za m'mitsinje mwako; udzagwa kuthengo koyera, sudzaunjikidwa, kapena kuoledwa; ndakupereka ukhale chakudya cha zilombo za padziko, ndi mbalame za kumlengalenga.
62Maf. 18.21Ndi onse okhala mu Ejipito adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, popeza anakhalira nyumba ya Israele mchirikizo wabango.
72Maf. 18.21Muja anakugwira ndi dzanja unathyoka, ndi kulasa mapewa ao onse; ndi muja anakutsamira unathyoka, ndi kuwagwedeza ziuno zao zonse.
8Chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Taona, ndikudzera ndi lupanga, ndi kukulikhira munthu ndi nyama.
9Ndi dziko la Ejipito lidzakhala lopasuka ndi labwinja; ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, popeza anati, Mtsinjewo ndi wanga, ndinaulenga ndine.
10Ezk. 30.12Chifukwa chake taona, nditsutsana ndi iwe ndi mitsinje yako, ndipo ndidzasandutsa dziko la Ejipito likhale lopasuka konse, ndi labwinja, kuyambira ku Migidoli mpaka ku nsanja ya Siyene kufikira malire a Kusi.
11Silidzapitamo phazi la munthu, kapena phazi la nyama losapitamo, losakhalamo anthu zaka makumi anai.
12Ezk. 30.12Ndipo ndidzasandutsa dziko la Ejipito labwinja pakati pa maiko a mabwinja; ndi mizinda yake pakati pa mizinda yopasuka idzakhala yabwinja zaka makumi anai; ndipo ndidzamwaza Aejipito mwa amitundu, ndi kuwabalalitsa m'maiko.
13Yer. 46.26Pakuti atero Ambuye Yehova, Zitatha zaka makumi anai ndidzasonkhanitsa Aejipito kumitundu ya anthu kumene anamwazikirako;
14Yer. 46.26ndipo ndidzabweza undende wa Ejipito, ndi kuwabwezera kudziko la Patirosi, kudziko la kubadwa kwao, ndi komweko adzakhala ufumu wopepuka.
15Udzakhala wopepuka wa maufumu onse, sudzadzikwezanso pa amitundu; ndipo ndidzawachepsa, kuti asachitenso ufumu pa amitundu.
16Yes. 30.2-3Ndipo sudzakhalanso chotama cha nyumba ya Israele, kukumbutsa mphulupulu, pakuwatembenukira kuwatsata; motero adzadziwa kuti Ine ndine Ambuye Yehova.
17Ndipo kunali chaka cha makumi awiri mphambu zisanu ndi ziwiri mwezi woyamba, tsiku loyamba la mwezi, anandidzera mau a Yehova, akuti,
18Yer. 27.6Wobadwa ndi munthu iwe, Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni anachititsa ankhondo ake ntchito yaikulu yoponyana ndi Tiro; mitu yonse inachita dazi, ndi mapewa onse ananyuka; koma analibe kulandira mphotho ya ku Tiro, iye kapena ankhondo ake, pa ntchito anagwirayo;
19chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Taona, ndidzapereka dziko la Ejipito kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni; ndipo adzachoka nao aunyinji ake, nadzafunkha ndi kulanda zake, ndizo mphotho ya khamu lake.
20Yer. 25.9Ndamninkha dziko la Ejipito chombwezera ntchito yake, popeza anandigwirira ntchito, ati Ambuye Yehova.
21 Mas. 132.17; Ezk. 24.27 Tsiku ilo ndidzameretsera nyumba ya Israele nyanga; ndipo ndidzakutsegulira pakamwa pakati pao; motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.