MLALIKI 4 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Matsoka ndi mavuto a moyo uno

1 Mlal. 5.8 Ndinabweranso tsono ndi kupenyera nsautso zonse zimachitidwa kunja kuno; ndipo taona, misozi ya otsenderezedwa, koma analibe wakuwatonthoza; ndipo akuwatsendereza anali ndi mphamvu koma iwowa analibe wakuwatonthoza.

2Yob. 3.17-22Ndipo ndinatama akufa atatha kufa kupambana amoyo omwe alipobe;

3inde yemwe sanabadwe konse aposa onse awiriwo popeza sanaone ntchito yoipa yochitidwa kunja kuno.

4Ndiponso ndinapenyera mavuto onse ndi ntchito zonse zompindulira bwino, kuti chifukwa cha zimenezi anansi ake achitira munthu nsanje. Ichinso ndi chabe ndi kungosautsa mtima.

5Chitsiru chimanga manja ake, ndipo chidya nyama yakeyake.

6Miy. 15.16-17Dzanja limodzi lodzala pali mtendere liposa manja awiri oti thoo pali vuto ndi kungosautsa mtima.

7Pamenepo ndinabwera ndi kupenyera zachabe kunja kuno.

8Miy. 27.20Pali mmodzi palibe wachiwiri; inde, alibe mwana ngakhale mbale; koma ntchito yake yonse ilibe chitsiriziro, ngakhale diso lake silikhuta chuma. Samati, Ndigwira ntchito ndi kumana moyo wanga zabwino chifukwa cha yani? Ichinso ndi chabe, inde, vuto lalikulu.

9Awiri aposa mmodzi; pakuti ali ndi mphotho yabwino m'ntchito zao.

10Pakuti akagwa, wina adzautsa mnzake; koma tsoka wakugwa wopanda womnyamutsa.

11Ndiponso awiri akagona limodzi afunditsana; koma mmodzi pa yekha kodi adzafunditsidwa bwanji?

12Ndipo wina akamgonjetsa mmodziyo, awiri adzachilimika; ndipo chingwe cha nkhosi zitatu sichiduka msanga.

13Mnyamata wosauka ndi wanzeru apambana mfumu yokalamba ndi yopusa, imene sifunanso kulangidwa mwambo.

14Pakuti atuluka m'nyumba yandende kulowa ufumu; komanso yemwe abadwa m'dziko lake asauka.

15Ndinapenyera anthu onse amoyo akuyenda kunja kuno, kuti anali ndi mwana, wachiwiri, amene adzalowa m'malo mwake.

16Anthu onse sawerengeka, ngakhale onsewo anawalamulira; koma amene akudza m'mbuyo sadzakondwera naye. Ichinso ndi chabe ndi chosautsa mtima.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help