EZEKIELE 6 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Aneneratu motsutsa mapiri a Israele

1Ndipo mau a Yehova anandidzera, kuti,

2Ezk. 36.1Wobadwa ndi munthu iwe, lozetsa nkhope yako kumapiri a Israele, uwanenere,

3Lev. 26.30nunene, Mapiri a Israele inu, tamverani mau a Yehova Mulungu: Atero Yehova Mulungu kwa mapiri ndi zitunda, kwa mitsinje ndi zigwa, Taonani, Ine ndikufikitsirani lupanga, ndipo ndidzaononga misanje yanu.

4Ndi maguwa anu a nsembe adzakhala opasuka, ndi zoimiritsa zanu zadzuwa zidzasweka; ndipo ndidzagwetsa ophedwa anu pamaso pa mafano anu.

5Ndipo ndidzaika mitembo ya ana a Israele pamaso pa mafano anu, ndi kumwaza mafupa anu mozungulira maguwa anu a nsembe.

6Pokhala inu ponse mizinda idzapasuka, ndi misanje idzakhala yabwinja; kuti maguwa anu a nsembe akhale opasuka ndi mabwinja, ndi mafano anu asweke nalekeke, ndi zoimiritsa zanu zadzuwa zilikhidwe, ndi ntchito zanu zifafanizidwe.

7Ndi ophedwa adzagwa pakati panu, motero mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

8Koma ndidzasiyapo otsala, popeza mudzakhala nao ena akupulumuka lupanga mwa amitundu pobalalitsidwa inu m'maiko maiko.

9Yob. 42.6; Mas. 78.40Pamenepo akupulumuka anu adzandikumbukira Ine kwa amitundu kumene anatengedwa ndende, kuti ndasweka ndi mtima wao wachigololo wolekana ndi Ine, ndi maso ao achigololo akutsata mafano ao; ndipo iwo adzakhala onyansa pamaso pao pa iwo eni, chifukwa cha zoipa anazichita m'zonyansa zao zonse.

10Ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, sindinanene chabe kuti ndidzawachitira choipa ichi.

11Atero Yehova Mulungu, Omba manja ako, ponda ndi phazi lako, nuti, Kalanga ine, chifukwa cha zonyansa zoipa zonse za nyumba ya Israele; pakuti adzagwa ndi lupanga, ndi njala, ndi mliri.

12Ezk. 5.13Wokhala kutali adzafa ndi mliri, wokhala pafupi adzagwa ndi lupanga; koma wotsala ndi kuzingidwa adzafa ndi njala; momwemo ndidzawakwaniritsira ukali wanga.

13Ezk. 6.7; Hos. 4.13Ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova, pokhala ophedwa ao pakati pa mafano ao, pozinga maguwa ao a nsembe, pa zitunda zonse zazitali, pamwamba pa mapiri onse, ndi patsinde pa mitengo yogudira yonse, ndi patsinde pa thundu aliyense wagudugudu, pomwe adapereka zonunkhira zokoma kwa mafano ao onse.

14Yes. 5.25Ndipo ndidzawatambasulira dzanja langa, ndi kulisandutsa dziko bwinja ndi lopasuka, koposa chipululu cha ku Ribula mokhalamo iwo monse; ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help