DANIELE 12 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Nthawi ya chimaliziro, mau otsekedwa

1 Yes. 26.20-21; Dan. 10.13, 21; Mat. 24.21; Luk. 10.20; Aro. 11.26; Afi. 4.3; Chiv. 16.18 Ndipo nthawi yomweyi adzauka Mikaele kalonga wamkulu wakutumikira ana a anthu a mtundu wako; ndipo padzakhala nthawi ya masautso, siinakhale yotere kuyambira mtundu wa anthu kufikira nthawi yomwe ija; ndipo nthawi yomweyo anthu ako adzapulumutsidwa, yense amene ampeza wolembedwa m'buku.

2Mat. 25.46; Yoh. 5.28-29Ndipo ambiri a iwo ogona m'fumbi lapansi adzauka, ena kunka kumoyo wosatha, ndi ena kumanyazi ndi mnyozo wosatha.

3Mala. 2.6; Mat. 13.43; Yak. 5.20Ndipo aphunzitsi adzawala ngati kunyezimira kwa thambo; ndi iwo otembenuza ambiri atsate chilungamo ngati nyenyezi kunthawi za nthawi.

4Chiv. 10.4; 22.10Koma iwe Daniele, tsekera mau awa, nukomere chizindikiro buku, mpaka nthawi ya chimaliziro; ambiri adzathamanga chauko ndi chauko, ndi chidziwitso chidzachuluka.

5Pamenepo ine Daniele ndinapenya, ndipo taonani, anaimapo awiri ena, wina m'mphepete mwa mtsinje tsidya lino, ndi mnzake m'mphepete mwa mtsinje tsidya lija.

6Dan. 10.5Ndipo wina anati kwa munthu wovala bafuta, wokhala pamwamba pamadzi a mumtsinje, Chimaliziro cha zodabwitsa izi chidzafika liti?

7Ndipo ndinamva munthuyo wovala bafuta wokhala pamwamba pamadzi a mumtsinje, nakweza dzanja lake lamanja ndi lamanzere kumwamba, nalumbira pali Iye wokhala ndi moyo kosatha, kuti zidzachitika nthawi, ndi nthawi zina, ndi nusu; ndipo atatha kumwaza mphamvu ya anthu opatulikawo zidzatha izi zonse.

8Ndinachimva ichi, koma osachizindikira; pamenepo ndinati Mbuye wanga, chitsiriziro cha izi nchiyani?

9Dan. 12.4Ndipo anati, Pita Daniele; pakuti mauwo atsekedwa, nakhomeredwa chizindikiro mpaka nthawi ya chitsiriziro.

10Zek. 13.9Ambiri adzadzitsuka ndi kudziyeretsa, nadzayesedwa ndi moto; koma oipa adzachita moipa; ndipo palibe mmodzi wa oipa adzazindikira; koma aphunzitsi ndiwo adzazindikira.

11Dan. 8.11Ndipo kuyambira nthawi yoti idzachotsedwa nsembe yachikhalire, ndipo chidzaimika chonyansa chakupululutsa, adzakhalanso masiku chikwi chimodzi mphambu mazana awiri kudza makumi asanu ndi anai.

12Wodala iye amene ayembekeza, nafikira kumasiku chikwi chimodzi mphambu mazana atatu kudza makumi atatu ndi asanu.

13Koma iwe, muka mpaka chimaliziro; pakuti udzapumula, nudzaima m'gawo lako masiku otsiriza.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help