1 Deut. 6.20, 23 Mulungu, tidamva m'makutu mwathu, makolo athu anatisimbira,
za ntchitoyo mudaichita masiku ao, masiku akale.
2 Deut. 7.1 Inu munapirikitsa amitundu ndi dzanja lanu,
koma iwowa munawaoka;
munasautsa mitundu ya anthu, ndipo munawaingitsa.
3 Deut. 8.17 Pakuti sanalande dziko ndi lupanga lao,
ndipo mkono wao sunawapulumutse.
Koma dzanja lanu lamanja, ndi mkono wanu,
ndi kuunika kwa nkhope yanu.
Popeza munakondwera nao,
4Inu ndinu mfumu yanga, Mulungu;
lamulirani chipulumutso cha Yakobo.
5Mwa Inu tidzakankhira pansi otsutsana nafe,
m'dzina lanu tidzapondereza akutiukira ife.
6 Hos. 1.7 Pakuti uta wanga,
ndipo lupanga langa silingandipulumutse.
7Koma Inu munatipulumutsa kwa iwo akutsutsana nafe,
ndipo akudana nafe, mudawachititsa manyazi.
8 Yer. 9.24; Aro. 2.17 Mwa Mulungu tidzitamanda tsiku lonse,
ndipo dzina lanu tidzaliyamika kosatha.
9Koma mwatitaya, ndi kutinyazitsa;
ndipo simutuluka nao makamu a nkhondo athu.
10 Yos. 7.8, 12 Mutibwereretsa kuthawa otisautsa,
ndipo akudana nafe adzifunkhira okha.
11 Aro. 8.36 Mwatipereka ngati nkhosa zoyenera kuzidya;
ndipo mwatibalalitsa mwa amitundu.
12 Yes. 52.3-4 Mugulitsa anthu anu kwachabe,
ndipo mtengo wake simupindula nao.
13 Deut. 28.37 Mutisandutsa chotonza kwa anzathu,
ndi choseketsa ndi cholalatitsa iwo akutizinga.
14Mutiika tikhale onyozeka mwa amitundu,
ndi kuti anthu atipukusire mitu.
15Tsiku lonse chimpepulo changa chikhala pamaso panga,
ndipo manyazi a pankhope panga andikuta.
16Chifukwa cha mau a wotonza wochitira mwano;
chifukwa cha mdani ndi wobwezera chilango.
17Zonsezi zatigwera; koma sitinakuiwalani,
ndipo sitinachite monyenga m'pangano lanu.
18 Mas. 119.51, 157 Mtima wathu sunabwerere m'mbuyo,
ndipo m'mayendedwe athu sitinapatuke m'njira yanu;
19mungakhale munatithyola mokhala zilombo,
ndi kutiphimba nao mthunzi wa imfa.
20Tikadaiwala dzina la Mulungu wathu,
ndi kutambasulira manja athu kwa mulungu wachilendo;
21 Yer. 17.10 Mulungu sakadasanthula ichi kodi?
Pakuti adziwa zinsinsi za mtima.
22 Aro. 8.36 Koma, chifukwa cha Inu, tiphedwa tsiku lonse;
tiyesedwa ngati nkhosa zakuzipha.
23 Mas. 44.9 Galamukani, mugoneranji, Ambuye?
Ukani, musatitaye chitayire.
24 Mas. 88.14 Mubisiranji nkhope yanu,
ndi kuiwala kuzunzika ndi kupsinjika kwathu?
25 Mas. 119.25 Pakuti moyo wathu waweramira kufumbi,
pamimba pathu pakangamira dziko lapansi.
26Ukani, tithandizeni,
tiomboleni mwa chifundo chanu.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.