ZEKARIYA Mau Oyamba - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu
Mau OyambaBukuli lili ndi zigawo ziwiri: Gawo loyamba ndi mau amene mneneri adalalikira kuyambira chaka cha 520 BC. Zekariya akulongosola zimene adaziwona m'masomphenya ndipo akuwachenjeza anthuwo nawalimbitsa mtima kuti akonzenso Kachisi komanso mzinda wa Yerusalemu. Iwo ayenera adziyeretsa popeza Yehova adzawadalitsa (1—8). Gawo lachiwiri ndi kaundula wa mauneneri osiyanasiyana onena za kubwera kwa Mesiya ndipo tsiku la chiweruzo (9—14).Za mkatimuMau oyamba 1.1—8.23Mau a Yehova aimba mlandu mitundu ina ya anthu 9.1-8Mau ena olonjeza zabwino 9.9—14.21