1 MBIRI 12 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Amphamvu anadza kwa Davide namtsata pomlonda Saulo

1 1Sam. 27.2-6 Anadzawo kwa Davide ku Zikilagi, akali chitsekedwere chifukwa cha Saulo mwana wa Kisi, ndi awa; ndiwo mwa amphamvuwo omthandiza kunkhondo.

2Ower. 20.16Anakoka mauta; naponya miyala, naponya mivi ndi uta ndi dzanja lamanja ndi lamanzere lomwe; ndiwo a abale ake a Saulo, Abenjamini.

3Mkulu wao ndiye Ahiyezere, ndi Yowasi, ana a Semaa wa ku Gibea; ndi Yeziyele, ndi Peleti, ana a Azimaveti; ndi Beraka, ndi Yehu wa ku Anatoti,

4ndi Isimaya wa ku Gibiyoni, wamphamvu mwa makumi atatuwo ndi woyang'anira makumi atatuwo, ndi Yeremiya, ndi Yahaziele, ndi Yohanani, ndi Yozabadi wa ku Gedera,

5Eluzai, ndi Yerimoti, ndi Bealiya, ndi Semariya, ndi Sefatiya wa ku Harufi,

6Elikana, ndi Isiya, ndi Azarele, ndi Yowezere, ndi Yasobeamu ndiwo Akora;

7ndi Yowela, ndi Zebadiya, ana a Yerohamu wa ku Gedori.

82Sam. 2.18Ndi Agadi ena anapatukira kwa Davide ku linga la m'chipululu, ngwazi zamphamvu zozerewera nkhondo, zogwira chikopa ndi mkondo; nkhope zao zikunga nkhope za mikango, ndi liwiro lao longa la ngoma mumapiri:

9Ezere mkulu wao, wachiwiri Obadiya, wachitatu Eliyabu,

10wachinai Misimana, wachisanu Yeremiya,

11wachisanu ndi chimodzi Atai, wachisanu ndi chiwiri Eliyele,

12wachisanu ndi chitatu Yohanani, wachisanu ndi chinai Elizabadi,

13wakhumi Yeremiya, wakhumi ndi chimodzi Makibanai.

14Awa a ana a Gadi, anali atsogoleri a nkhondo; wamng'ono wa iwo anayang'anira zana limodzi, ndi wamkulu wa iwo anayang'anira chikwi chimodzi.

15Yos. 3.15Awa ndi omwe aja anaoloka Yordani mwezi woyamba, atadzala kusefukira magombe ake onse; nathawitsa onse okhala m'zigwa kum'mawa ndi kumadzulo.

16Ndipo anadza ena a ana a Benjamini ndi Yuda kulinga kwa Davide.

17Ndipo Davide anatuluka kukomana nao, nayankha, nanena nao, Ngati mwandidzera mwamtendere kundithandiza, mtima wanga udzalumikizana nanu; koma ngati mwafika kundipereka kwa adani anga, popeza m'manja mwanga mulibe chiwawa, Mulungu wa makolo athu achione ndi kuchilanga.

181Sam. 25.6; 2Sam. 17.25Pamenepo mzimu unavala Amasai, ndiye wamkulu wa makumi atatuwo, nati iye, Ndife anu, Davide, tivomerezana nanu mwana wa Yese inu: mtendere, mtendere ukhale ndi inu, ndi mtendere ukhale ndi athandizi anu; pakuti Mulungu wanu akuthandizani. Ndipo Davide anawalandira, nawaika akulu a magulu.

191Sam. 29.2-9Ena a Manase omwe anapatukira kwa Davide, muja iye anadza ndi Afilisti koponyana nkhondo ndi Saulo, koma sanawathandize; popeza akalonga a Afilisti, atachita upo, anamuuza achoke, ndi kuti, Adzapatukira kwa mbuye wake Saulo ndi kutisandulikira.

20Pomuka iye ku Zikilagi anapatukira kwa iye a Manase: Adina, ndi Yozabadi, ndi Yediyaele, ndi Mikaele, ndi Yozabadi, ndi Elihu, ndi Ziletai, akulu a zikwi a ku Manase.

211Sam. 30.1, 9-10Ndipo anathandiza Davide aponyane nalo gulu la achifwamba, pakuti onse ndiwo ngwazi zamphamvu, nakhala atsogoleri m'khamu la nkhondo.

22Pakuti nthawi yomweyo anadza kwa Davide kumthandiza, mpaka kunali nkhondo yaikulu, ngati nkhondo ya Mulungu.

Akulu omponya Davide mfumu ku Hebroni

23 2Sam. 2.3-4 Ndipo kuwerenga kwa akulu okonzekeratu kunkhondo, anadzawo kwa Davide ku Hebroni, kupambukitsa ufumu wa Saulo ukhale wake, monga mwa mau a Yehova, ndi uku.

24Ana a Yuda akunyamula zikopa ndi mikondo ndiwo zikwi zisanu ndi chimodzi mphambu mazana asanu ndi atatu, okonzekeratu kunkhondo.

25A ana a Simeoni ngwazi zamphamvu za nkhondo zikwi zisanu ndi ziwiri mphambu zana limodzi.

26A ana a Levi zikwi zinai mphambu mazana asanu ndi limodzi.

27Ndipo Yehoyada, ndiye mtsogoleri wa nyumba ya Aroni, ndi pamodzi naye zikwi zitatu mphambu mazana asanu ndi awiri;

282Sam. 8.17ndi Zadoki, ndiye mnyamata, ngwazi yamphamvu, ndi a nyumba ya kholo lake akulu makumi awiri mphambu awiri.

292Sam. 2.8-9Ndi a ana a Benjamini, abale a Saulo, zikwi zitatu; pakuti mpaka pomwepo ochuluka a iwowa anaumirira nyumba ya Saulo.

30Ndi a ana a Efuremu zikwi makumi awiri mphambu mazana asanu ndi atatu, ngwazi zamphamvu, anthu omveka m'nyumba za makolo ao.

31Ndipo a hafu la fuko la Manase zikwi khumi mphambu zisanu ndi zitatu, otchulidwa maina ao kuti adzalonge Davide mfumu.

32Ndi a ana a Isakara, anthu akuzindikira nyengo, akudziwa zoyenera Israele kuzichita, akulu ao ndiwo mazana awiri; ndi abale ao onse anapenyerera pakamwa pao.

33A Zebuloni akutuluka kukhamu, opangira nkhondo, monga mwa zida zilizonse za nkhondo, zikwi makumi asanu, akusunga malongosoledwe a nkhondo ndi mtima wosatekeseka.

34Ndi a Nafutali atsogoleri chikwi chimodzi, ndi pamodzi nao ogwira zikopa ndi mikondo zikwi makumi atatu mphambu zisanu ndi ziwiri.

35Ndi a Adani akupangira nkhondo zikwi makumi awiri mphambu zisanu ndi zitatu kudza mazana asanu ndi limodzi.

36Ndi a Asere akutuluka kukhamu, akupangira nkhondo, zikwi makumi anai.

37Ndi tsidya lija la Yordani a Arubeni, ndi Agadi, ndi hafu la fuko la Manase, ndi zina zilizonse za khamu kuchita nazo nkhondo, zikwi zana limodzi ndi makumi awiri.

38Onsewa, ndiwo anthu a nkhondo akusunga malongosoledwe a nkhondo, anadza ku Hebroni ndi mtima wangwiro kudzamlonga Davide mfumu ya Aisraele onse; ndi onse otsala a Israele omwe anali a mtima umodzi kumlonga Davide ufumu.

39Ndipo anali komweko kwa Davide masiku atatu kudya ndi kumwa, popeza abale ao anazikonzeratu.

40Ndiponso akuyandikizana nao mpaka Isakara ndi Zebuloni ndi Nafutali anabwera nao mkate osenzetsa abulu, ndi ngamira, ndi nyuru, ndi ng'ombe, zakudya zaufa, ndi nchinchi zankhuyu, ndi nchinchi zamphesa, ndi vinyo, ndi mafuta, ndi ng'ombe, ndi nkhosa zochuluka; pakuti munali chimwemwe mu Israele.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help