1 Mas. 24.3-4 Indedi Mulungu achitira Israele zabwino,
iwo a mtima wa mbee.
2Koma ine, ndikadagwa;
mapazi anga akadaterereka.
3 Yer. 12.1 Pakuti ndinachitira nsanje odzitamandira,
pakuona mtendere wa oipa.
4Pakuti palibe zomangira pakufa iwo,
ndi mphamvu yao njolimba.
5 Yob. 21.7, 9 Savutika monga anthu ena;
sasautsika monga anthu ena.
6Chifukwa chake kudzikuza kunga unyolo pakhosi pao;
achivala chiwawa ngati malaya.
7Kunenepa kwao kutuzulitsa maso ao,
malingaliro a mitima yao asefukira.
8 Hos. 7.16 Achita zaphwete nalankhula moipa za kusautsa,
alankhula modzitama.
9Pakamwa pao anena zam'mwamba,
ndipo lilime lao liyendayenda m'dziko lapansi.
10 Mas. 75.8 Chifukwa chake anthu ake amabwera kudza kuno,
ndipo chikho chodzala ndi madzi achigugudiza.
11 1Sam. 2.3 Namati, Akachidziwa bwanji Mulungu?
Kodi Wam'mwambamwamba ali nayo nzeru?
12 Mas. 73.3 Tapenyani, oipa ndi awa;
ndipo pokhazikika chikhazikikire aonjezerapo pa chuma chao.
13 Yob. 34.9; Mas. 26.6 Indedi, ndinayeretsa mtima wanga kwachabe,
ndipo ndinasamba m'manja mosalakwa.
14Popeza andisautsa tsiku lonse,
nandilanga mamawa monse,
15ndikadati, Ndidzafotokozera chotere,
taonani, ndikadachita chosakhulupirika ndi mbadwo wa ana ako.
16Pamene ndinayesa kudziwitsa ichi,
ndinavutika nacho;
17 Mas. 37.38 mpaka ndinalowa m'zoyera za Mulungu,
ndi kulingalira chitsiriziro chao.
18Indedi muwaika poterera,
muwagwetsa kuti muwaononge.
19Ha? M'kamphindi ayesedwa bwinja;
athedwa konse ndi zoopsa.
20Monga anthu atauka, apepula loto;
momwemo, Inu Ambuye, pakuuka
mudzapeputsa chithunzithunzi chao.
21Pakuti mtima wanga udawawa,
ndipo ndinalaswa mu impso zanga;
22 Miy. 30.2 ndinali wam'thengo, wosadziwa kanthu;
ndinali ngati nyama pamaso panu.
23 Mas. 63.8 Koma ndikhala ndi Inu chikhalire,
mwandigwira dzanja langa la manja.
24 Mas. 32.8 Mudzanditsogolera ndi uphungu wanu,
ndipo mutatero, mudzandilandira mu ulemerero.
25 Afi. 3.8 Ndili ndi yani Kumwamba, koma Inu?
Ndipo padziko lapansi palibe wina wondikonda koma Inu.
26 Mas. 84.2 Likatha thupi langa ndi mtima wanga,
Mulungu ndiye thanthwe la mtima wanga,
ndi cholandira changa chosatha.
27 Eks. 34.15 Pakuti, taonani, iwo okhala patali ndi Inu adzaonongeka;
muononga onse akupembedza kwina, kosiyana ndi Inu.
28Koma ine, kundikomera kuyandikiza kwa Mulungu.
Ndimuyesa Ambuye Yehova pothawirapo ine,
kuti ndifotokozere ntchito zanu zonse.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.