YOBU 31 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

1 Mat. 5.28 Ndinapangana ndi maso anga,

potero ndipenyerenji namwali?

2Pakuti gawo la Mulungu lochokera kumwamba,

ndi cholowa cha Wamphamvuyonse chochokera m'mwambamo nchiyani?

3Si ndizo chionongeko cha wosalungama,

ndi tsoka la ochita mphulupulu?

4 2Mbi. 16.9; Yer. 32.19 Nanga sapenya njira zanga,

ndi kuwerenga moponda mwanga monse?

5Ngati ndinayanjana nalo bodza,

ndi phazi langa linathamangira chinyengo;

6 Dan. 5.27 andiyese ndi muyeso wolingana,

kuti Mulungu adziwe ungwiro wanga.

7 Mlal. 11.9 Ngati phazi langa linapatuka m'njira,

ndi mtima wanga unatsata maso anga?

Ngati chilema chamamatira manja anga?

8 Lev. 26.16; Yoh. 4.37 Ndibzale ine nadye wina,

ndi zondimerera ine zizulidwe.

9Ngati mtima wanga wakopeka ndi mkazi,

ngati ndalalira pa khomo la mnzanga,

10 2Sam. 12.11 mkazi wanga aperere wina;

wina namuike kumbuyo.

11 Lev. 20.10 Pakuti icho ndi choipitsitsa,

ndicho mphulupulu yoyenera oweruza anene mlandu wake.

12Pakuti ndicho moto wakunyeka mpaka chionongeko,

ndi chakuzula zipatso zanga zonse.

13Ngati ndapeputsa mlandu wa kapolo wanga,

kapena wa mdzakazi wanga,

potsutsana nane iwo,

14ndidzatani ponyamuka Mulungu?

Ndipo pondizonda Iye ndidzamnyankha chiyani?

15Kodi Iye amene anandilenga ine m'mimba

sanamlenge iyenso?

Sindiye mmodzi anatiumba m'mimba?

16Ngati ndakaniza aumphawi chifuniro chao,

kapena kutopetsa maso a amasiye,

17kapena kudya nthongo yanga ndekha,

osadyako mwana wamasiye;

18(pakuti kuyambira ubwana wanga analeredwa

ndi ine monga ndi atate;

ndipo ndinakhala nkhoswe ya wamasiye chibadwire ine.)

19Ngati ndinaona wina alinkutayika wopanda chovala,

kapena kuti wosowa alibe chofunda;

20ngati ziuno zake sizinandiyamike,

ngati sanafunde ubweya wa nkhosa zanga;

21ngati ndinasamulira ana amasiye dzanja langa,

popeza ndinaona thandizo langa kuchipata;

22libanthuke phewa langa paphalo,

ndi dzanja langa liduke pagwangwa.

23 Yes. 13.6 Pakuti tsoka lochokera kwa Mulungu linandiopsa,

ndi chifukwa cha ukulu wake sindinakhoza kanthu.

24 Mrk. 10.24; 1Tim. 6.17 Ngati ndayesa golide chiyembekezo changa,

ndi kunena ndi golide woyengetsa,

ndiwe chikhazikitso changa;

25 Mas. 62.10; Miy. 11.28 ngati ndinakondwera popeza chuma changa nchachikulu,

ndi dzanja langa lapeza zochuluka;

26ngati ndalambira dzuwa lilikuwala,

kapena mwezi ulikuyenda monyezimira;

27ndi mtima wanga wakopeka m'tseri,

ndi pakamwa panga padapsompsona dzanja langa;

28ichinso ndi mphulupulu yoyenera oweruza

kunena mlandu wake;

pakuti ndikadakana Mulungu ali m'mwamba.

29 Miy. 17.5 Ngati ndakondwera nalo tsoka la wondida,

kapena kudzitukula pompeza choipa;

30 Mat. 5.44; Aro. 12.14 ndithu sindinalole m'kamwa mwanga muchimwe,

kupempha motemberera moyo wake.

31Ngati amuna a m'hema mwanga sanati,

ndani adzapeza munthu wosakhuta nyama yomgawira Yobu?

32 Gen. 19.2-3; Aro. 12.13 Mlendo sakagona pakhwalala,

koma ndinatsegulira wam'njira pakhomo panga.

33 Gen. 3.8, 12 Ngati ndakwirira zolakwa zanga monga Adamu,

ndi kubisa mphulupulu yanga m'chifuwa mwanga;

34popeza ndinaopa unyinji waukulu,

ndi chipepulo cha mafuko chinandiopsetsa;

potero ndinakhala chete osatuluka pakhomo panga.

35Ha! Ndikadakhala naye wina wakundimvera,

chizindikiro changa sichi, Wamphamvuyonse andiyankhe;

mwenzi ntakhala nao mau akundineneza

analemberawo mdani wanga!

36Ndithu ndikadawasenza paphewa panga,

ndi kudzimangirira awa ngati korona.

37Ndikadamfotokozera chiwerengo cha mopondamo mwanga,

ndikadamsenderera Iye ngati kalonga.

38Ngati minda yanga ifuula monditsutsa,

ndi nthumbira zake zilira pamodzi;

39 Yak. 5.4 ngati ndadya zipatso zake wopanda ndalama.

Kapena kutayitsa eni ake moyo wao;

40imere minga m'malo mwa tirigu,

ndi dawi m'malo mwa barele.

Mau a Yobu atha.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help