1 MBIRI 6 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Adzukulu a Levi

1 Gen. 46.11; Num. 26.57 Ana a Levi: Geresomo, Kohati, ndi Merari.

2Ndi ana a Kohati: Amuramu, Izihara, ndi Hebroni, ndi Uziyele.

3Eks. 6.20; Lev. 10.1, 12Ndi ana a Amuramu: Aroni, ndi Mose, ndi Miriyamu. Ndi ana a Aroni: Nadabu, ndi Abihu, Eleazara, ndi Itamara.

4Eleazara anabala Finehasi, Finehasi anabala Abisuwa,

5ndi Abisuwa anabala Buki, ndi Buki anabala Uzi,

6ndi Uzi anabala Zerahiya, ndi Zerahiya anabala Meraiyoti,

7Meraiyoti anabala Amariya, ndi Amariya anabala Ahitubi,

82Sam. 15.27ndi Ahitubi anabala Zadoki, ndi Zadoki anabala Ahimaazi,

9ndi Ahimaazi anabala Azariya, ndi Azariya anabala Yohanani,

101Maf. 6ndi Yohanani anabala Azariya (ndiye amene anachita ntchito ya nsembe m'nyumba anaimanga Solomoni mu Yerusalemu),

11ndi Azariya anabala Amariya, ndi Amariya anabala Ahitubi,

12ndi Ahitubi anabala Zadoki, ndi Zadoki anabala Salumu,

13Mas. 22.4-5ndi Salumu anabala Hilikiya, ndi Hilikiya anabala Azariya,

14ndi Azariya anabala Seraya, ndi Seraya anabala Yehozadaki,

152Maf. 25.8-21ndi Yehozadaki analowa undende muja Yehova anatenga ndende Yuda ndi Yerusalemu ndi dzanja la Nebukadinezara.

16 Eks. 6.16 Ana a Levi: Geresomo, Kohati ndi Merari.

17Ndipo maina a ana a Geresomo ndi awa: Libini, ndi Simei.

18Ndipo ana a Kohati ndiwo Amuramu, ndi Izihara, ndi Hebroni, ndi Uziyele.

19Ana a Merari: Mali ndi Musi. Ndi mabanja a Alevi monga mwa nyumba za makolo ao ndi awa.

20Wa Geresomo: Libini mwana wake, Yahati mwana wake, Zima mwana wake,

21Yowa mwana wake, Ido mwana wake, Zera mwana wake, Yeterai mwana wake.

22Ana a Kohati: Aminadabu mwana wake, Kora mwana wake, Asiri mwana wake,

23Elikana mwana wake, ndi Ebiyasafu mwana wake, ndi Asiri mwana wake,

24Tahati mwana wake, Uriyele mwana wake, Uziya mwana wake, ndi Shaulo mwana wake.

25Ndi ana a Elikana: Amasai, ndi Ahimoti.

26Elikana: ana a Elikana Zofai mwana wake, ndi Nahati mwana wake,

27Eliyabu mwana wake, Yerohamu mwana wake, Elikana mwana wake.

28Ndi ana a Samuele: woyamba Yowele, ndi wachiwiri Abiya.

29Ana a Merari: Mali, Libini mwana wake, Simei mwana wake, Uza mwana wake,

30Simea mwana wake, Hagiya mwana wake, Asaya mwana wake.

A udindo wa kuimba

31 1Mbi. 16.4-6 Ndipo iwo aja Davide anawaimika a udindo wa nyimbo m'nyumba ya Yehova, litafikira kupumula likasalo, ndi awa.

32Ndipo anatumikira ndi kuimba pakhomo pa Kachisi wa chihema chokomanako mpaka Solomoni adamanga nyumba ya Yehova mu Yerusalemu, naimirira mu utumiki wao monga mwa malongosoledwe ao.

33Ndipo oimirirawo, ndi ana ao, ndi awa: a ana a Akohati, Hemani woimbayo, mwana wa Yowele, mwana wa Samuele,

34mwana wa Elikana, mwana wa Yerohamu, mwana wa Eliyele, mwana wa Towa,

35mwana wa Zufu, mwana wa Elikana, mwana wa Mahati, mwana wa Amasai,

36mwana wa Elikana, mwana wa Yowele, mwana wa Azariya, mwana wa Zefaniya,

37mwana wa Tahati, mwana wa Asiri, mwana wa Ebiyasafu, mwana wa Kora,

38mwana wa Izihara, mwana wa Kohati, mwana wa Levi, mwana wa Israele.

39Ndi mbale wake Asafu wokhala ku dzanja lake lamanja, ndiye Asafu mwana wa Berekiya, mwana wa Simea,

40mwana wa Mikaele, mwana wa Baaseiya, mwana wa Malikiya,

41mwana wa Etini, mwana wa Zera, mwana wa Adaya,

42mwana wa Etani, mwana wa Zima, mwana wa Simei,

43mwana wa Yahati, mwana wa Geresomo, mwana wa Levi.

44Ndi ku dzanja lamanzere abale ao ana a Merari: Etani mwana wa Kisi, mwana wa Abidi, mwana wa Maluki,

45mwana wa Hasabiya, mwana wa Amaziya, mwana wa Hilikiya,

46mwana wa Amizi, mwana wa Bani, mwana wa Semeri,

47mwana wa Mali, mwana wa Musi, mwana wa Merari, mwana wa Levi.

48Ndi abale ao Alevi anaikidwa achite za utumiki zilizonse za chihema cha nyumba ya Mulungu.

Ansembe mwa Alevi

49 Eks. 30.7, 10; Lev. 1.7, 9 Koma Aroni ndi ana ake ankafukiza paguwa la nsembe yopsereza, ndi paguwa la nsembe yofukiza, chifukwa cha ntchito yonse ya malo opatulika kwambiri, ndi kuchitira Israele chowatetezera, monga mwa zonse Mose mtumiki wa Mulungu adawauza.

501Mbi. 6.3Ndipo ana a Aroni ndiwo Eleazara mwana wake, Finehasi mwana wake, Abisuwa mwana wake,

51Buki mwana wake, Uzi mwana wake, Zerahiya mwana wake,

52Meraiyoti mwana wake, Amariya mwana wake, Ahitubi mwana wake,

53Zadoki mwana wake, Ahimaazi mwana wake.

Midzi ya Alevi

54Pokhala pao tsono monga mwa madera ao m'malire mwao ndi awa: kwa ana a Aroni a mabanja a Akohati, pakuti maere oyamba adagwera iwowa,

55kwa iwo anapereka Hebroni m'dziko la Yuda, ndi podyetsa pake pozungulira pake;

56koma minda ya mzinda ndi midzi yake anapatsa Kalebe mwana wa Yefune.

57Yos. 21.10-31Ndi kwa ana a Aroni anapereka mizinda yopulumukirako: Hebroni, ndi Libina ndi mabusa ake, ndi Yatiri, ndi Esitemowa ndi mabusa ake.

58Yos. 21.15Ndi Hileni ndi mabusa ake, ndi Debiri ndi mabusa ake,

59ndi Asani ndi mabusa ake, ndi Betesemesi ndi mabusa ake;

60ndi ku fuko la Benjamini Geba ndi mabusa ake, ndi Alemeti ndi mabusa ake, ndi Anatoti ndi mabusa ake. Mizinda yao yonse mwa mabanja ao ndiyo mizinda khumi ndi itatu.

61Ndipo otsala a ana a Kohati analandira mwa maere, motapa pa mabanja a fuko, pa hafu la fuko la Manase, mizinda khumi.

62Ndi kwa ana a Geresomo monga mwa mabanja ao, motapa pa fuko la Isakara, ndi pa fuko la Asere, ndi pa fuko la Nafutali, ndi pa fuko la Manase mu Basani, mizinda khumi ndi itatu.

63Ana a Merari analandira mwa maere monga mwa mabanja ao, motapa pa fuko la Rubeni, ndi pa fuko la Gadi, ndi pa fuko la Zebuloni, mizinda khumi ndi iwiri.

64Ndipo ana a Israele anapatsa Alevi mizinda ndi mabusa ao.

65Ndipo anapatsa mwamaere, motapa pa fuko la ana a Yuda, ndi pa fuko la Simeoni, ndi pa fuko la ana a Benjamini, mizinda iyi yotchulidwa maina ao.

66Ndi mabanja ena a ana a Kohati anali nayo mizinda ya malire ao, yotapa pa fuko la Efuremu.

67Yos. 21.21Ndipo anawapatsa mizinda yopulumukiramo: Sekemu ndi mabusa ake ku mapiri a Efuremu, Gezere ndi mabusa ake,

68ndi Yokomeamu ndi mabusa ake, ndi Betehoroni ndi mabusa ake,

69ndi Ayaloni ndi mabusa ake, ndi Gatirimoni ndi mabusa ake,

70ndi motapa pa hafu la fuko la Manase, Anere ndi mabusa ake, ndi Bileamu ndi mabusa ake, kwa otsala a mabanja a ana a Kohati.

71Yos. 21.27-33Ana a Geresomo analandira motapa pa mabanja a hafu la fuko la Manase, Golani mu Basani ndi mabusa ake, ndi Asitaroti ndi mabusa ake;

72ndi motapa pa fuko la Isakara, Kedesi ndi mabusa ake, Daberati ndi mabusa ake,

73ndi Ramoti ndi mabusa ake, ndi Anemu ndi mabusa ake;

74ndi motapa pa fuko la Asere, Masala ndi mabusa ake, ndi Abidoni ndi mabusa ake,

75ndi Hukoki ndi mabusa ake, ndi Rehobu ndi mabusa ake;

76ndi motapa pa fuko la Nafutali, Kedesi mu Galileya ndi mabusa ake, ndi Hamoni ndi mabusa ake, ndi Kiriyataimu ndi mabusa ake.

77Amerari (otsala a Alevi) analandira, motapa pa fuko la Zebuloni, Rimoni ndi mabusa ake, Tabori ndi mabusa ake;

78ndi tsidya lija la Yordani kum'mawa kwa Yeriko analandira, motapa pa fuko la Rubeni, Bezeri m'chipululu ndi mabusa ake, ndi Yahazi ndi mabusa ake,

79ndi Kedemoti ndi mabusa ake, ndi Mefaati ndi mabusa ake;

80ndi motapa m'fuko la Gadi, Ramoti mu Giliyadi ndi mabusa ake, ndi Mahanaimu ndi mabusa ake,

81ndi Hesiboni ndi mabusa ake, ndi Yazere ndi mabusa ake.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help