1 PETRO Mau Oyamba - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Mau Oyamba Kalata yoyamba ya Petro analembera Akhristu, amene panopa akutchedwa “anthu osankhika a Mulungu”, amene anabalalika m'dera lonse la dziko limene masiku ano limatchedwa Turkey. Cholinga chenicheni cha kalatayi ndicho kuwalimbikitsa owerengawo, amene amakumana ndi mazunzo osiyanasiyana ndipo amasautsidwa chifukwa cha chikhulupiriro chao. Olembayo akuchita izi powakumbutsa awerengiwo za Uthenga Wabwino wa Yesu Khristu umene imfa yake, kuuka kwake ndi lonjezano la kubweranso kwake, zinawapatsa chiyembekezo. Chifukwa chake iwowa ayenera kuvomereza zakuti adzazunzika ndipo apirire m'masautso. Iwo atsimikizike kuti kuzunzidwaku ndiko mayeso a kulimba kwa chikhulupiriro chao ndipo adzalandira mphotho “pa vumbulutso la Yesu Khristu” (1.7).Kuphatikizapo chilimbikitso chimenechi m'nthawi ya mazunzo, olembayo akuwalimbikitsa awerengi ake kuti akhale m'moyo monga anthu amene ali ake a Khristu.Za mkatimuMau oyamba 1.1-2Kukumbutsa za chipulumutso cha Mulungu 1.3-12Kulimbikitsana za khalidwe la moyo woyera 1.13—2.10Udindo wa Mkhristu pa nthawi ya mazunzo 2.11—4.19Kudzichepetsa ndi utumiki wa Chikhristu 5.1-11Mau omaliza 5.12-14
Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help