DEUTERONOMO 17 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

1 Deut. 15.21 Musamaphera Yehova Mulungu wanu nsembe ya ng'ombe, kapena nkhosa, yokhala nacho chilema, kapena chilichonse choipa; pakuti chinyansira Yehova Mulungu wanu.

2Akapeza pakati panu, m'mudzi wanu wina umene anakupatsani Yehova Mulungu wanu, wamwamuna kapena wamkazi wakuchita chili choipa pamaso pa Yehova Mulungu wanu, ndi kulakwira chipangano chake,

3nakatumikira milungu ina, naigwadira iyo, kapena dzuwa, kapena mwezi, kapena wina wa khamu la kuthambo, losauza Ine;

4ndipo akakuuzani, nimudamva, pamenepo muzifunsira, ndipo taonani, chikakhala choonadi, choti nzenizeni, chonyansachi chachitika mu Israele;

5pamenepo mutulutse mwamunayo kapena mkaziyo, anachita choipacho, kunka naye ku zipata zanu, ndiye wamwamuna kapena wamkazi; ndipo muwaponye miyala, kuti afe.

6Deut. 19.15; Mat. 18.16; 2Ako. 13.1; Aheb. 10.28Pakamwa pa mboni ziwiri kapena zitatu amuphe iye amene akuti afe; asamuphe pakamwa pa mboni imodzi.

7Liyambe kumgwera dzanja la mboniyo kumupha; pamenepo dzanja la anthu onse. Potero muzichotsa choipacho pakati panu.

8 2Mbi. 19.10 Ukakukanikani mlandu pouweruza, ndiwo wakunena zamwazi, kapena zakutsutsana, kapena zakupandana, ndiyo milandu yakutengana m'midzi mwanu; pamenepo muziuka ndi kukwera kunka ku malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha;

9nimufike kwa ansembe, Alevi, ndi kwa woweruza wa m'masiku awo; nimufunsire; ndipo adzakufotokozerani maweruzidwe ake.

10Ndipo muchite monga momwe ananena mau akufotokozeraniwo, ku malo amene Yehova adzawasankha; nimusamalire kuchita monga mwa zonse akulangizanizi.

11Monga momwe anena malamulo akulangizani, ndi monga mwa chiweruzo akufotokozerani muchite; mau akufotokozerani musawapatukire kulamanja kapena kulamanzere.

12Koma munthu wakuchita modzikuza, osamvera wansembe wokhala chilili kutumikirako pamaso pa Yehova Mulungu wanu, kapena woweruza, munthuyo afe; ndipo muchotse choipacho kwa Israele.

13Ndipo anthu onse adzamva ndi kuchita mantha, osachitanso modzikuza.

Za kusankha mfumu ndi zomuyenera

14 1Sam. 8.5 Mutakalowa m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani, ndi kulilandira lanulanu, ndi kukhalamo; ndipo mukanena, Tidziikire mfumu, monga amitundu onse akutizinga;

151Sam. 9.16mumuiketu mfumu yanu imene Yehova Mulungu wanu adzaisankha; wina pakati pa abale anu mumuike mfumu yanu; simuyenera kudziikira mlendo, wosakhala mbale wanu.

161Maf. 4.26Koma asadzichulukitsire akavalo iye, kapena kubwereretsa anthu anke ku Ejipito, kuti achulukitse akavalo; popeza Yehova anati nanu, Musamabwereranso njira iyi.

171Maf. 11.3Ndipo asadzichulukitsire akazi, kuti ungapatuke mtima wake; kapena asadzichulukitsire kwambiri siliva ndi golide.

181Maf. 11.12Ndipo kudzali, pakukhala iye pa mpando wachifumu wa ufumu wake, adzilemberere chofanana cha chilamulo ichi m'buku, achitenge pa ichi chili pamaso pa ansembe Alevi;

19Mas. 119.97-98ndipo azikhala nacho, nawerengemo masiku onse a moyo wake; kuti aphunzire kuopa Yehova Mulungu wake, kusunga mau onse a chilamulo ichi ndi malemba awa, kuwachita;

20kuti mtima wake usadzikuze pa abale ake, ndi kuti asapatukire lamulolo, kulamanja kapena kulamanzere; kuti achuluke masiku ake, mu ufumu wake, iye ndi ana ake pakati pa Israele.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help