YEREMIYA 26 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Yeremiya aneneratu za kupasuka kwa Kachisi ndi Yerusalemu. Atsutsidwapo afe

1Poyamba kukhala mfumu Yehoyakimu mwana wake wa Yosiya, mfumu ya Yuda, panadza mau awa ochokera kwa Yehova, kuti,

2Mac. 20.27Yehova atero: Ima m'bwalo la nyumba ya Yehova, ndi kunena kwa mizinda yonse ya Yuda, imene imadza kudzagwadira m'nyumba ya Yehova, mau onse amene ndikuuza iwe kuti unene kwa iwo; usasiyepo mau amodzi.

3Yer. 36.3; Yon. 3.8-9Kapena adzamvera, nadzatembenuka, yense kusiya njira yake yoipa; kuti ndileke choipa, chimene ndinati ndiwachitire chifukwa cha kuipa kwa ntchito zao.

4Deut. 28.15Ndipo iwe uziti kwa iwo, Yehova atero: Ngati simudzandimvera Ine kuyenda m'chilamulo changa, chimene ndachiika pamaso panu,

5kumvera mau a atumiki anga aneneri, amene ndituma kwa inu, pouka mamawa ndi kuwatuma iwo, koma simunamvere;

6Yer. 7.12pamenepo ndidzayesa nyumba iyi ifanane ndi Silo, ndipo ndidzayesa mzinda uwu chitemberero cha kwa mitundu yonse ya dziko lapansi.

7Ndipo ansembe ndi aneneri ndi anthu onse anamva Yeremiya alinkunena mau awa m'nyumba ya Yehova.

8Ndipo panali, pamene Yeremiya anatha kunena mau onse amene Yehova anamuuza iye kuti anene kwa anthu onse, ansembe ndi aneneri ndi anthu onse anamgwira iye, ndi kuti, Udzafa ndithu.

9Bwanji mwanenera m'dzina la Yehova, kuti, Nyumba iyi idzafanana ndi Silo, mzinda uwu udzakhala bwinja lopanda wokhalamo? Ndipo anthu onse anamsonkhanira Yeremiya m'nyumba ya Yehova.

10Ndipo pamene akulu a Yuda anamva zimenezi, anakwera kutuluka kunyumba ya mfumu kunka kunyumba ya Yehova; ndipo anakhala pa khomo la Chipata Chatsopano cha nyumba ya Yehova.

11Yer. 38.4Ndipo ansembe ndi aneneri ananena kwa akulu ndi kwa anthu onse, kuti, Munthu uyu ayenera kufa; pakuti wanenera mzinda uwu monga mwamva ndi makutu anu.

12Pamenepo Yeremiya ananena kwa akulu onse ndi kwa anthu onse, kuti, Yehova anandituma ine ndinenere nyumba iyi ndi mzinda uwu mau onse amene mwamva.

13Yer. 7.3Chifukwa chake tsopano konzani njira zanu ndi machitidwe anu, ndi kumvera mau a Yehova Mulungu wanu; ndipo Yehova adzaleka choipa chimene ananenera inu.

14Yer. 38.5Koma ine, taonani, ndili m'manja anu; mundichitire ine monga mokomera ndi moyenera m'maso anu.

15Koma mudziwe ndithu kuti, ngati mudzandipha ine, mudzadzitengera nokha mwazi wosachimwa, ndi pa mzinda uwu, ndi pa okhalamo ake; pakuti mwa ntheradi Yehova wandituma kwa inu kuti ndinene mau onse awa m'makutu anu.

16Pamenepo akulu ndi anthu onse anati kwa ansembe ndi kwa aneneri, Munthu uyu sayenera kufa: pakuti watinenera ife m'dzina la Yehova Mulungu wathu.

17Mac. 5.34-39Ndipo anauka akulu ena a m'dziko, nati kwa msonkhano wa anthu, kuti,

18Mik. 1.1; 3.12Mika Mmoreseti ananenera masiku a Hezekiya mfumu ya Yuda; ndipo iye ananena kwa anthu onse a Yuda, kuti, Yehova wa makamu atero: Ziyoni adzalimidwa ngati munda, Yerusalemu adzakhala miunda, ndi phiri la nyumba longa misanje ya nkhalango.

192Mbi. 32.26; Mac. 5.39Kodi Hezekiya mfumu ya Yuda ndi Yuda wonse anamupha iye konse? Kodi sanamuope Yehova, napembedzera Yehova, ndipo Yehova analeka choipa chimene ananenera iwo? Chotero tidzaichitira miyoyo yathu choipa chachikulu.

20Ndipo panalinso munthu amene ananenera m'dzina la Yehova, Uriya mwana wake wa Semaya wa ku Kiriyati-Yearimu; ndipo iye ananenera mzinda uwu ndi dziko lino monga mwa mau onse a Yeremiya;

21ndipo pamene Yehoyakimu mfumu, ndi amphamvu ake onse, ndi akulu onse, anamva mau ake, mfumu inafuna kumupha iye; koma pamene Uriya anamva, anaopa, nathawa, nanka ku Ejipito;

22ndipo Yehoyakimu mfumu anatuma anthu ku Ejipito, Elinatani mwana wake wa Akibori, ndi anthu ena pamodzi ndi iye, anke ku Ejipito;

23ndipo anamtulutsa Uriya mu Ejipito, nanka naye kwa Yehoyakimu mfumu; amene anamupha ndi lupanga, naponya mtembo wake m'manda a anthu achabe.

24Yer. 39.14Koma dzanja la Ahikamu mwana wa Safani linali ndi Yeremiya, kuti asampereke m'manja a anthu kuti amuphe.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help