1Ndipo Mose anaitana Aisraele onse, nanena nao, Tamverani, Israele, malemba ndi maweruzo ndinenawa m'makutu mwanu lero, kuti muwaphunzire, ndi kusamalira kuwachita.
2Eks. 19.5Yehova Mulungu wathu anapangana nafe chipangano mu Horebu.
3Yehova sanachite chipangano ichi ndi makolo athu, koma ndi ife, ife amene tili ndi moyo tonsefe pano lero.
4Yehova ananena ndi inu popenyana maso m'phirimo, ali pakati pa moto,
5Eks. 20.21(ndinalinkuima pakati pa Yehova ndi inu muja, kukulalikirani mau a Yehova; popeza munachita mantha chifukwa cha moto, osakwera m'phirimo) ndi kuti:
6 Eks. 20.2-17 Ine ndine Yehova Mulungu wako amene ndinakutulutsa m'dziko la Ejipito, m'nyumba ya ukapolo.
7Usakhale nayo milungu ina koma Ine ndekha.
8Usadzipangire iwe wekha fano losema, kapena chifaniziro chilichonse cha zinthu za m'thambo la kumwamba, kapena za m'dziko lapansi, kapena za m'madzi a pansi padziko;
9usazipembedzere izo, usazitumikire izo; chifukwa Ine Yehova Mulungu wako ndine Mulungu wansanje, wakulanga ana chifukwa cha atate wao, kufikira mbadwo wachitatu ndi wachinai wa iwo amene akudana ndi Ine;
10ndi kuchitira chifundo anthu zikwi, a iwo amene akondana ndi Ine nasunga malamulo anga.
11Usatchule dzina la Yehova Mulungu wako pachabe; chifukwa Yehova sadzamuyesa iye wosachimwa amene atchula pachabe dzina lakelo.
12Samalira tsiku la Sabata likhale lopatulika, monga Yehova Mulungu wako anakulamulira.
13Masiku asanu ndi limodzi uzigwiritsa ntchito, ndi kuchita ntchito zako zonse;
14koma tsiku lachisanu ndi chiwiri ndilo Sabata la Yehova Mulungu wako; usamagwira ntchito iliyonse, iwe, kapena mwana wako wamwamuna, kapena mwana wako wamkazi, kapena wantchito wako wamwamuna, kapena wantchito wako wamkazi, kapena ng'ombe yako, kapena bulu wako, kapena zoweta zako zilizonse, kapena mlendo wokhala m'mudzi mwako; kuti wantchito wako wamwamuna ndi wantchito wako wamkazi apumule monga iwe mwini.
15Ndipo uzikumbukira kuti unali kapolo m'dziko la Ejipito, ndi kuti Yehova Mulungu wako anakutulutsako ndi dzanja lamphamvu ndi mkono wotambasuka; chifukwa chake Yehova Mulungu wako anakulamulira kusunga tsiku la Sabata.
16Lemekeza atate wako ndi amai ako, monga Yehova Mulungu wako anakulamulira; kuti masiku ako achuluke, ndi kuti chikukomere, m'dziko limene Yehova Mulungu wako akupatsa iwe.
17Usaphe.
18Usachite chigololo.
19Usabe.
20Usamnamizire mnzako.
21Usasirire mkazi wake wa mnzako; usakhumbe nyumba yake ya mnzako, munda wake, kapena wantchito wake wamwamuna, kapena wantchito wake wamkazi, ng'ombe yake, kapena bulu wake, kapena kanthu kalikonse ka mnzako.
22 Eks. 24.12 Yehova ananena mau awa kwa msonkhano wanu wonse, m'phirimo ali pakati pa moto, pamtambo, pamdima bii, ndi mau aakulu; osaonjezapo kanthu. Ndipo anawalembera pa magome awiri amiyala, nandipatsa awa.
23Ndipo kunali, pamene munamva liu lotuluka pakati pa mdima, potentha phiri ndi moto, munayandikiza kwa ine, ndiwo mafumu onse a mafuko anu ndi akulu anu;
24Eks. 19.19ndipo munati, Taonani, Yehova Mulungu wathu anationetsa ulemerero wake, ndi ukulu wake, ndipo tidamva liu lake ali pakati pa moto; tapenya lero lino kuti Mulungu anena ndi munthu, ndipo akhala ndi moyo.
25Ndipo tsopano tiferenji? Popeza moto waukulu uwu udzatitha. Tikaonjeza kumva mau a Yehova Mulungu wathu, tidzafa.
26Deut. 4.33Pakuti ndaniyo, wa zamoyo zonse adamva mau a Mulungu wamoyo wakunena ali pakati pa moto, monga ife nakhala ndi moyo?
27Yandikizani inu, ndi kumva zonse Yehova Mulungu wathu adzati; ndipo inu munene ndi ife zonse zimene Yehova Mulungu wathu adzanena ndi inu; ndipo ife tidzazimva ndi kuzichita.
28Ndipo Yehova anamva mau a kunena kwanu, pamene munanena ndi ine; ndipo Yehova anati kwa ine, Ndidamva mau a kunena kwao kwa anthu awa, amene ananena ndi iwe; chokoma chokhachokha adanenachi.
29Mas. 81.13; Mat. 23.37Ha? Mwenzi akadakhala nao mtima wotere wakundiopa Ine, ndi kusunga malamulo anga masiku onse, kuti chiwakomere iwo ndi ana ao nthawi zonse!
30Muka, nuti nao, Bwererani ku mahema anu.
31Koma iwe, uime kuno ndi Ine, ndinene ndi iwe malamulo onse, ndi malemba, ndi maweruzo, amene uziwaphunzitsa, kuti awachite m'dziko limene ndiwapatsa likhale laolao.
32Potero muzisamalira kuchita monga Yehova Mulungu wanu anakulamulirani; musamapatuka kulamanzere kapena kulamanja.
33Luk. 1.6Muziyenda m'njira yonse imene Yehova Mulungu wanu anakulamulirani, kuti mukakhale ndi moyo, ndi kuti chikukomereni, ndi kuti masiku anu achuluke m'dziko limene mudzakhala nalo lanulanu.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.