YOBU 24 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

1 Mac. 1.7 Wamphamvuyonse alekeranji kuikiratu nyengo?

Ndi iwo omdziwa alekeranji kudziwa masiku ake?

2 Deut. 19.14 Alipo akusendeza malire;

alanda gulu la zoweta, nazidyetsa.

3 Deut. 24.17 Akankhizira kwao bulu wa amasiye,

atenga ng'ombe ya mfedwa ikhale chikole.

4Apatukitsa aumphawi m'njira;

osauka a padziko abisala pamodzi.

5Taonani, ngati mbidzi za m'chipululu

atulukira kuntchito zao, nalawirira nkufuna chakudya;

chipululu chiwaonetsera chakudya cha ana ao.

6Atema dzinthu zao m'munda;

natola khunkha m'munda wampesa wa woipa.

7 Deut. 24.12-13 Agona amaliseche usiku wonse opanda chovala,

alibe chofunda pachisanu.

8Avumbwa ndi mvula kumapiri,

nafukata thanthwe posowa pousapo.

9Akwatula wamasiye kubere,

natenga chikole chovala cha osauka;

10momwemo ayenda amaliseche opanda chovala,

nasenza mtolo wa dzinthu ali ndi njala.

11M'kati mwa malinga a iwo aja ayenga mafuta;

aponda mphesa moponderamo, namva ludzu.

12M'mzinda waukulu anthu abuula alinkufa;

ndi moyo wa iwo olasidwa ufuula;

koma Mulungu sasamalira choipacho.

13Iwo ndiwo amene apikisana nako kuunika,

sadziwa njira zake, Sasunga mayendedwe ake.

14 Mas. 10.8 Kukacha auka wambanda, napha wosauka ndi waumphawi;

ndi usiku asanduka mbala.

15 Miy. 7.9-10 Ndipo diso la wachigololo liyembekezera chisisira,

ndi kuti, Palibe diso lidzandiona;

navala chophimba pankhope pake.

16 Yoh. 3.20 Kuli mdima aboola nyumba,

usana adzitsekera,

osadziwa kuunika.

17Pakuti iwo onse auyesa m'mawa mthunzi wa imfa;

pakuti adziwa zoopsa za mthunzi wa imfa.

18Atengedwa ngati choyandama pamadzi;

gawo lao litembereredwa padziko;

sadzalunjikanso njira ya minda yampesa.

19Chilala ndi dzuwa zitha madzi a chipale chofewa,

momwemo manda achita nao ochimwa.

20 Miy. 10.7 M'mimba mudzamuiwala;

mphutsi zidzamudya mokondwera.

Sadzamkumbukiranso;

ndipo chosalungama chidzathyoledwa ngati mtengo.

21Alusira chumba wosabala,

osamchitira wamasiye chokoma.

22Mulungu awakhalitsa amphamvu mwa mphamvu yake;

iwo aukanso m'mene anayesa kuti sadzakhala ndi moyo.

23 Miy. 15.3 Awalola akhale osatekeseka, ndipo alimbikapo;

koma maso ake ali panjira zao.

24Akwezeka; m'kamphindi kuli zii;

inde atsitsidwa, achotsedwa monga ena onse,

adulidwa ngati tirigu ngala zake.

25Ndipo ngati si kutero, anditsutsa ndani kuti ndili wabodza,

ndi kuyesa mau anga opanda pake?

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help