1Ndipo Iye ananena ndi Mose, Ukwere kudza kwa Yehova, iwe ndi Aroni, Nadabu ndi Abihu, ndi akulu a Israele makumi asanu ndi awiri; ndipo mugwadire pakudza kutali;
2ndipo Mose yekha ayandikire kwa Yehova; koma asayandikire iwowa; ndi anthunso asakwere naye.
3Eks. 19.8Ndipo Mose anadza nafotokozera anthu mau onse a Yehova, ndi maweruzo onse; ndipo anthu onse anavomera pamodzi, nati, Mau onse walankhula Yehova tidzachita.
4Ndipo Mose analembera mau onse a Yehova, nalawira kuuka mamawa, namanga guwa la nsembe patsinde paphiri, ndi zoimiritsa khumi ndi ziwiri, kwa mafuko khumi ndi awiri a Israele.
5Ndipo anatuma ana a Israele a misinkhu ya anyamata, ndiwo anapereka nsembe zopsereza, naphera Yehova nsembe zamtendere, za ng'ombe.
6Aheb. 9.18-19Ndipo Mose anagawa mwaziwo, nathira wina m'zotengera, nawaza wina paguwa la nsembe
7Ndipo anatenga buku la Chipangano, nawerenga m'makutu a anthu; ndipo iwo anati, Zonse zimene Yehova walankhula tidzachita, ndi kumvera.
8Aheb. 9.19-20Ndipo Mose anatenga mwaziwo, nawaza pa anthu, nati Taonani mwazi wa chipangano, chimene Yehova anachita nanu, kunena za mau awa onse.
9Ndipo Mose ndi Aroni, Nadabu ndi Abihu, ndi akulu a Israele makumi asanu ndi awiri anakwerako;
10ndipo anapenya Mulungu wa Israele; ndipo pansi pa mapazi ake panali ngati mayalidwe oyera a miyala yasafiro, ndi ngati thupi la thambo loti mbee.
11Koma sanatulutse dzanja lake pa akulu a ena a Israele; ndipo anapenya Mulungu, nadya, namwa.
12 Eks. 31.18 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Ukwere kudza kwa Ine m'phiri muno, nukhale pompano; ndipo ndidzakupatsa magome amiyala, ndi chilamulo ndi malamulo ndawalembera kuti uwalangize.
13Ndipo anauka Mose, ndi Yoswa mtumiki wake; ndipo Mose anakwera m'phiri la Mulungu.
14Ndipo anati kwa akulu, Tilindeni kuno kufikira tidzabwera kwa inu; ndipo taonani, Aroni ndi Huri ali nanu; munthu akakhala ndi mlandu abwere kwa iwowa.
15Ndipo Mose anakwera m'phirimo, ndi mtambo unaphimba phirilo.
16Ndipo ulemerero wa Yehova unakhalabe paphiri la Sinai, ndi mtambo unaliphimba masiku asanu ndi limodzi; ndipo tsiku lachisanu ndi chiwiri Iye ali m'kati mwa mtambo anaitana Mose.
17Aheb. 12.29Ndipo maonekedwe a ulemerero wa Yehova anali ngati moto wonyeketsa pamwamba paphiri, pamaso pa ana a Israele.
18Ndipo Mose analowa m'kati mwa mtambo, nakwera m'phirimo; ndipo Mose anakhala m'phiri masiku makumi anai usana ndi usiku.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.