YESAYA 16 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

1 2Maf. 3.4 Tumizani inu anaankhosa kwa wolamulira wa dziko kuchokera ku Sela kunka kuchipululu, mpaka kuphiri la mwana wamkazi wa Ziyoni.

2Pakuti ana aakazi a Mowabu adzakhala pa madooko a Arinoni, ngati mbalame zoyendayenda, ngati chisa chofwanchuka.

3Chitani uphungu, weruzani chiweruziro; yesa mthunzi wako monga usiku pakati pa usana; bisa opirikitsidwa, osawulula woyendayenda.

4Opirikitsidwa a Mowabu akhale ndi iwe, khala iwe chomphimba pamaso pa wofunkha; pakuti kumpambapamba kwalekeka, kufunkha kwatha, opondereza atsirizika m'dziko.

5Dan. 7.14, 27; Luk. 1.33Ndipo mpando wachifumu udzakhazikika m'chifundo, ndimo wina adzakhala pamenepo m'zoona, m'chihema cha Davide, nadzaweruza, nadzafunitsa chiweruziro, nadzafulumira kuchita chilungamo.

6 Zef. 2.10 Ife tinamva kunyada kwa Mowabu, kuti iye ali wonyada ndithu; ngakhale kudzitama kwake, ndi kunyada kwake ndi mkwiyo wake; matukutuku ake ali achabe.

7Chifukwa chake Mowabu adzakuwa chifukwa cha Mowabu, onse adzakuwa; chifukwa cha maziko a Kiri-Haresefi mudzalira maliro, osautsidwa ndithu.

8Pakuti minda ya ku Hesiboni yalefuka, ndi mpesa wa ku Sibima; ambuye a mitundu athyolathyola mitengo yosankhika yake; iwo anafikira ngakhale ku Yazere, nayendayenda m'chipululu; nthambi zake zinatasa, zinapitirira panyanja.

9Chifukwa chake ndidzalira ndi kulira kwa Yazere, chifukwa cha mpesa wa Sibima, ndidzakukhathamiza ndi misozi yanga, iwe Hesiboni ndi Eleyale; chifukwa kuti pa zipatso zako za malimwe, ndi pa masika ako, mfuu wankhondo wagwera.

10Ndipo chikondwerero ndi msangalalo zachotsedwa m'munda wopatsa zipatso; ndi m'minda ya mipesa simudzakhala kuimba, ngakhale phokoso losangalala; palibe woponda adzaponda vinyo m'moponderamo; ndaleketsa mfuu wa masika amphesa.

11Chifukwa chake m'mimba mwanga mulirira Mowabu, ngati mngoli, ndi za m'mtima mwanga zilirira Kiriheresi.

12Deut. 32.37-39; 1Maf. 18.29Ndipo padzakhala kuti pamene Mowabu adzadzionetsa yekha, ndi kudzitopetsa pamsanje, ndipo kufika kumalo ake oyera kudzapemphera, sadzapindulapo kanthu.

13Awa ndi mau amene Yehova adanena za Mowabu nthawi zapitazo.

14Koma tsopano Yehova wanena, nati, Zisanapite zaka zitatu monga zaka za wolembedwa ntchito, ulemerero wa Mowabu udzakhala wonyozeka, ndi khamu lalikulu lake, ndi otsala adzakhala ang'onong'ono ndi achabe.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help