FILEMONI 1 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

1 Aef. 3.1 Paulo, wandende wa Khristu Yesu, ndi Timoteo mbaleyo, kwa Filemoni wokondedwayo ndi wantchito mnzathu,

2Aro. 16.5; Akol. 4.17ndi kwa Afiya mlongoyo, ndi Arkipo msilikali mnzathu, ndi kwa Mpingo uli m'nyumba yako:

3Aef. 1.2Chisomo kwa inu ndi mtendere za kwa Mulungu Atate wathu ndi Ambuye Yesu Khristu.

4 Aef. 1.16 Ndiyamika Mulungu wanga nthawi zonse, ndi kukumbukira iwe m'mapemphero anga,

5Akol. 1.4pakumva za chikondi chako ndi chikhulupiriro uli nacho chakulinga kwa Ambuye Yesu, ndi kwa oyera mtima onse;

6kuti chiyanjano cha chikhulupiriro chako chikakhale champhamvu podziwa chabwino chilichonse chili mwa inu, cha kwa Khristu.

72Ako. 7.13Pakuti ndinali nacho chimwemwe chambiri ndi chisangalatso pa chikondi chako, popeza mitima ya oyera mtima yatsitsimuka mwa iwe, mbale.

Paulo apempherera kapolo wothawa wotembenuka mtima

8 1Ate. 2.6 Momwemo, ndingakhale ndili nako kulimbika mtima kwakukulu mu Khristu kukulamulira chimene chiyenera,

9File. 1.1koma makamaka ndidandaulira mwa chikondi, pokhala wotere, Paulo nkhalamba, ndipo tsopano wandendenso wa Khristu Yesu;

10Akol. 4.9; 1Ako. 4.15ndikudandaulira chifukwa cha mwana wanga, amene ndambala m'ndende, Onesimo,

11amene kale sanakupindulire, koma tsopano watipindulira bwino iwe ndi ine;

12amene ndi yemweyo ndakubwezera iwe, ndiye mtima weniweni wa ine.

13Afi. 2.30Ameneyo ndikadafuna ine kumsunga akhale nane, kuti m'malo mwako akadanditumikira ine m'ndende za Uthenga Wabwino:

142Ako. 9.7koma wopanda kudziwa mtima wako sindinafune kuchita kanthu; kuti ubwino wako usakhale monga mokakamiza, komatu mwaufulu.

15Gen. 45.5, 8Pakuti kapena anasiyanitsidwa ndi iwe kanthawi chifukwa cha ichi, ndi kuti udzakhala naye nthawi zonse;

161Tim. 6.2osatinso monga kapolo, koma woposa kapolo, mbale wokondedwa, makamaka ndi ine, koma koposa nanga ndi iwe, m'thupi, ndiponso mwa Ambuye.

17Ngati tsono undiyesa woyanjana nawe, umlandire iye monga ine mwini.

18Koma ngati anakulakwira kanthu, kapena wokongola kanthu, kanthu, kapena wakongola kanthu, undiwerengere ine kameneko;

19ine Paulo ndichilemba ndi dzanja langa, ndidzachibwezera ine; kuti ndisanene nawe kuti iwe ndiwe mangawa anga.

20Inde, mbale, ndikondwere nawe mwa Ambuye: utsitsimutse mtima wanga mwa Khristu.

212Ako. 7.16Pokhulupirira kumvera kwako ndikulembera iwe, podziwa kuti udzachitanso koposa chimene ndinena.

22Koma undikonzerenso pogona; pakuti ndiyembekeza kuti mwa mapemphero anu ndidzapatsidwa kwa inu.

23 Akol. 1.7 Epafra wandende mnzanga mwa Khristu Yesu akukupatsa moni;

24Mac. 12.25; 19.29; Akol. 4.14ateronso, Marko, Aristariko, Dema, Luka, antchito anzanga.

25 2Tim. 4.22 Chisomo cha Ambuye wathu Yesu Khristu chikhale pamodzi ndi mzimu wanu. Amen.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help