1 1Sam. 31.1-13 Afilisti tsono analimbana nkhondo ndi Israele; ndipo amuna a Israele anathawa pamaso pa Afilisti, nagwa ophedwa paphiri la Gilibowa.
2Ndipo Afilisti anaumirira kutsata Saulo ndi ana ake, ndi Afilistiwo anapha Yonatani, ndi Abinadabu, ndi Malikisuwa, ana a Saulo.
3Ndi nkhondoyi inamkulira Saulo, ndi amauta anampeza; ndipo anatenga nkhawa chifukwa cha amauta.
4Pamenepo Saulo anati kwa wonyamula zida zake, Solola lupanga lako, nundipyoze nalo, angafike osadulidwa awa ndi kundiseka. Koma wonyamula zida zake anakana, popeza anaopa kwambiri. Pomwepo Saulo anatenga lupanga lake, naligwera.
5Ndipo pamene wonyamula zida zake anaona kuti Saulo wafa, anagwera nayenso lupanga lake, nafa.
6Momwemo anafa Saulo, ndi ana ake atatu; ndi nyumba yake yonse idafa pamodzi.
7Ndipo pamene amuna onse a Israele okhala m'chigwamo anaona kuti anathawa, ndi kuti Saulo ndi ana ake adafa, anasiya mizinda yao, nathawa; nadza Afilisti, nakhala m'menemo.
8Ndipo m'mawa mwake anafika Afilisti kuvula za ophedwa, napeza Saulo ndi ana ake adagwa paphiri la Gilibowa.
9Ndipo anamvula natenga mutu wake, ndi zida zake, natumiza ku dziko la Afilisti pozungulirapo, kulalika m'mafano ao ndi mwa anthu.
10Ndipo anaika zida zake m'nyumba ya milungu yao, napachika mutu wake m'nyumba ya Dagoni.
11Ndipo onse a Yabesi-Giliyadi, atamva zonse Afilisti adachitira Saulo,
12anauka ngwazi zonse, nachotsa mtembo wa Saulo, ndi mitembo ya ana ake, nabwera nayo ku Yabesi, naika mafupa ao patsinde pa mtengo wathundu ku Yabesi, nasala masiku asanu ndi awiri.
131Sam. 13.13; 28.7Momwemo Saulo anafa, chifukwa cha kulakwa kwake analakwira Yehova, kulakwira mau a Yehova amene sanawasunge; ndiponso chifukwa cha kufunsira wobwebweta, kufunsirako,
142Sam. 3.9-10osafunsira kwa Yehova; chifukwa chake anamupha, napambutsira ufumu kwa Davide mwana wa Yese.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.