NUMERI 30 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Za chowinda chochita akazi

1Ndipo Mose ananena ndi akulu a mafuko a ana a Israele, nati, Chinthu anachilamulira Yehova ndi ichi:

2Lev. 27.2; Mas. 66.13-14; Mat. 14.9; Mac. 23.14Munthu akachitira Yehova chowinda, kapena akalumbira lumbiro ndi kumangira moyo wake chodziletsa, asaipse mau ake; azichita monga mwa zonse zotuluka m'kamwa mwake.

3Ndipo mkazi akachitira Yehova chowinda, nakadzimanga nacho chodziletsa, pokhala ali m'nyumba ya atate wake, mu unamwali;

4ndipo atate wake akamva chowinda chake, ndi chodziletsa chake anamanga nacho moyo wake, koma wakhala naye chete atate wake; pamenepo zowinda zake zonse zidzakhazikika, ndi chodziletsa chilichonse wamanga nacho moyo wake chidzakhazikika.

5Koma atate wake akamletsa tsiku lakumva iye; zowinda zake zonse, ndi zodziletsa zake zonse anamanga nazo moyo wake, sizidzakhazikika; ndipo Yehova adzamkhululukira, popeza atate wake anamletsa.

6Ndipo akakwatibwa naye mwamuna, pokhala ali nazo zowinda zake, kapena zonena zopanda pake za milomo yake, zimene anamanga nazo moyo wake;

7nakazimva mwamuna wake, nakakhala naye chete tsiku lakuzimva iye; pamenepo zowinda zake zidzakhazikika, ndi zodziletsa anamanga nazo moyo wake zidzakhazikika.

8Koma mwamuna wake akamletsa tsiku lakumva iye; pamenepo adzafafaniza chowinda chake anali nacho, ndi zonena zopanda pake za milomo yake, zimene anamanga nazo moyo wake; ndipo Yehova adzamkhululukira.

9Koma chowinda cha mkazi wamasiye, kapena mkazi wochotsedwa, zilizonse anamanga nazo moyo wake zidzamkhazikikira.

10Ndipo ngati anawinda m'nyumba ya mwamuna wake, kapena anamanga moyo wake ndi chodziletsa ndi kulumbirapo,

11ndipo mwamuna wake anamva, koma anakhala naye chete osamletsa, pamenepo zowinda zake zonse zidzakhazikika, ndi zodziletsa zonse anamanga nazo moyo wake zidzakhazikika.

12Koma ngati mwamuna wake anazifafanizadi tsiku lakuzimva iye, zonse zotuluka m'milomo yake kunena za zowinda zake, kapena za chodziletsa cha moyo wake sizidzakhazikika; mwamuna wake anafafaniza; ndipo Yehova adzamkhululukira iye.

13Chowinda chilichonse, ndi cholumbira chilichonse chodziletsa chakuchepetsa nacho moyo, mwamuna wake achikhazikira, kapena mwamuna wake achifafaniza.

14Koma mwamuna wake akhala naye chete tsiku ndi tsiku; pamenepo akhazikira zowinda zake zonse, kapena zodziletsa zake zonse, zili pa iye; wazikhazikitsa, popeza anakhala naye chete tsikuli anazimva iye.

15Koma akazifafaniza atatha kuzimva; pamenepo adzasenza mphulupulu yake.

16Awa ndi malemba amene Yehova analamulira Mose, a pakati pa mwamuna ndi mkazi wake, pakati pa atate ndi mwana wake wamkazi, akali namwali, m'nyumba ya atate wake.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help