2 SAMUELE 23 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Nyimbo yotsiriza ya Davide

1 1Sam. 16.12-13 Ndipo mau otsiriza a Davide ndi awa:

Atero Davide mwana wa Yese,

atero munthu wokwezedwa,

ndiye wodzozedwa wa Mulungu wa Yakobo,

ndi mwini nyimbo yokoma ya Israele.

2 2Pet. 1.21 Mzimu wa Yehova unalankhula mwa ine,

ndi mau ake anali pa lilime langa.

3Mulungu wa Israele anati,

Thanthwe la Israele linalankhula ndi ine;

kudzakhala woweruza anthu molungama;

woweruza m'kuopa Mulungu.

4 Ower. 5.31 Iye adzakhala ngati kuunika kwa m'mawa,

potuluka dzuwa, M'mawa mopanda mitambo;

pamene msipu uphuka kutuluka pansi,

chifukwa cha kuwala koyera, italeka mvula.

5 2Sam. 7.15-16 Zoonadi nyumba yanga siikhala yotere ndi Mulungu;

koma Iye anapangana ndi ine pangano losatha,

lolongosoka mwa zonse ndi losungika;

pakuti ichi ndi chipulumutso changa chonse,

ndi kufuma kwanga konse,

kodi sadzachimeretsa?

6Koma oipa onse adzakhala ngati minga yoyenera kuitaya,

pakuti siigwiridwa ndi dzanja;

7koma wakukhudza iyo adzikonzeratu chitsulo ndi luti la mkondo;

ndipo idzatenthedwa konse ndi moto m'malo mwao.

Angwazi a Davide(1Mbi. 11.10-41)

8Maina a ngwazi Davide anali nazo ndiwo: Yosebu-Basebeti Mtakemoni, mkulu wa akazembe; ameneyu ndiye Adino Mwezni wolimbana ndi mazana atatu ophedwa nthawi imodzi.

9Ndipo wotsatana naye Eleazara mwana wa Dodo mwana wa Mwahohi, mmodzi wa ngwazi zitatu zokhala ndi Davide pamene iwo anatonza Afilisti osonkhanidwa kunkhondo kumeneko, atachoka Aisraele;

10iye ananyamuka, nakantha Afilisti kufikira dzanja lake linalema, ndi dzanja lake lomamatika kulupanga; ndipo Yehova anachititsa chipulumutso chachikulu tsiku lija, ndipo anthu anabwera m'mbuyo mwake kukafunkha kokha.

111Mbi. 11.12-14Ndipo wotsatana naye ndiye Sama mwana wa Age Muharari. Ndipo Afilisti anasonkhana ali gulu pa Lehi pamene panali munda wamphodza; anthu nathawa Afilistiwo.

12Koma iyeyo anaima pakati pamundawo, nautchinjiriza, napha Afilistiwo. Ndipo Yehova anachititsa chipulumutso chachikulu.

13Ndipo atatu a mwa makamu atatu opambanawo, anatsika nafika kwa Davide nyengo ya kukolola m'phanga la ku Adulamu; ndi gulu la Afilisti linamanga zithando m'chigwa cha Refaimu.

14Pamenepo Davide anali m'linga, ndi boma la Afilisti linali mu Betelehemu.

15Ndipo Davide analakalaka nati, Ha! Wina akadandipatsa madzi a m'chitsime cha ku Betelehemu chili pachipatapo!

16Ndipo ngwazi zitatuzo zinapyola khamu la Afilisti, ndipo zinatunga madzi m'chitsime cha ku Betelehemu, cha pa chipatacho, nawatenga, nafika nao kwa Davide; koma iye sanafune kumwako, koma anawathira pansi kwa Yehova.

17Nati, Ndisachite ichi ndi pang'ono ponse, Yehova; ndimwe kodi mwazi wa anthu awa anapitawa ndi kutaya moyo wao? Chifukwa chake iye anakana kumwa. Izi anazichita ngwazi zitatuzi.

18Ndipo Abisai, mbale wa Yowabu, mwana wa Zeruya, anali wamkulu wa atatuwa. Iye natukula mkondo wake pa anthu mazana atatu nawapha, natenga dzina iye mwa atatuwa.

19Kodi iye sindiye waulemu mwa atatuwa? Chifukwa chake anali kazembe wao; ngakhale iyenso sadafikane ndi atatu oyamba.

20Ndipo Benaya, mwana wa Yehoyada, mwana wa ngwazi wa ku Kabizeeli amene anachita zamphamvu; iye anapha anthu awiri a Mowabu akunga mikango, natsikanso iye napha mkango m'mbuna nyengo ya chipale chofewa;

21ndipo anapha Mwejipito munthu wokongola, Mwejipito anali nao mkondo m'dzanja lake; koma iyeyo anatsikira kwa iye ndi ndodo, nasolola mkondowo m'dzanja la Mwejipito, namupha ndi mkondo wa iye mwini.

22Izi anachita Benaya mwana wa Yehoyada, natenga dzina mwa ngwazi zitatuzo.

23Iye ndiye waulemu koposa makumi atatuwo, koma sadafikane ndi atatu oyamba. Ndipo Davide anamuika kuyang'anira olindirira ake.

24Asahele mbale wa Yowabu anali wa makumi atatuwo; Elihanani mwana wa Dodo wa ku Betelehemu;

25Sama Mharodi, Elika Mharodi;

26Helezi Mpaliti, Ira mwana wa Ikesi Mtekowa.

27Abiyezere Mwanatoti, Mebunai Muhusa;

28Zalimoni Mwahohi, Maharai Mnetofa;

29Helebi mwana wa Baana Mnetofa, Itai mwana wa Ribai wa ku Gibea wa ana a Benjamini;

30Benaya Mpiratoni, Hidai wa ku timitsinje ta Gaasi;

31Abiyaliboni Mwarabati, Azimaveti Mbahurimi;

32Eliyaba Msaaliboni wa ana a Yaseni, Yonatani;

33Sama Muharari, Ahiyamu mwana wa Sarara Muharari;

34Elifeleti mwana wa Ahasibai, mwana wa Mmaaka, Eliyamu mwana wa Ahitofele Mgiloni;

35Heziro wa ku Karimele, Paarai Mwaraba;

36Igala mwana wa Natani wa ku Zoba, Bani Mgadi;

37Zeleki Mwamoni, Naharai Mbeeroti, onyamula zida za Yowabu mwana wa Zeruya;

38Ira Mwitiri, Garebu Mwitiri;

392Sam. 11.3, 6Uriya Muhiti; onse pamodzi anali makumi atatu mphambu asanu ndi awiri.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help