TITO 3 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

1 Aro. 13.1 Uwakumbutse iwo agonje kwa akulu, ndi aulamuliro, akhale omvera, okonzeka pa ntchito iliyonse yabwino;

2Aef. 4.31; Akol. 3.12asachitire mwano munthu aliyense, asakhale andeu, akhale aulere, naonetsere chifatso chonse pa anthu onse.

3Akol. 1.21Pakuti kale ifenso tinali opusa, osamvera, onyengeka, akuchitira ukapolo zilakolako ndi zokondweretsa za mitundumitundu, okhala m'dumbo ndi njiru, odanidwa, odana wina ndi mnzake.

4Tit. 2.11Koma pamene kukoma mtima, ndi chikondi cha pa anthu, cha Mpulumutsi wathu Mulungu zidanoneka,

5Yoh. 3.3, 5; 1Tim. 4.12zosati zochokera m'ntchito za m'chilungamo, zimene tidazichita ife, komatu monga mwa chifundo chake anatipulumutsa ife, mwa kutsuka kwa kubadwanso ndi makonzedwe a Mzimu Woyera,

6Yoh. 1.16amene anatsanulira pa ife mochulukira, mwa Yesu Khristu Mpulumutsi wathu;

7Aro. 8.17; Agal. 2.16kuti poyesedwa olungama ndi chisomo cha Iyetu, tikayesedwe olowa nyumba monga mwa chiyembekezo cha moyo wosatha.

8Okhulupirika mauwa, ndipo za izi ndifuna kuti ulimbitse mau, kuti iwo akukhulupirira Mulungu asamalire akhalebe atsogoleri a ntchito zabwino. Izi nzokoma ndi zopindulitsa anthu;

91Tim. 1.4koma pewa mafunso opusa, ndi mawerengedwe a mibadwo, ndi ndeu, ndi makani a pamalamulo; pakuti sizipindulitsa, ndipo zili zachabe.

10Mat. 18.17Munthu wopatukira chikhulupiriro, utamchenjeza kamodzi ndi kawiri, umkanize,

11Mac. 13.46podziwa kuti wotereyo wasandulika konse, nachimwa, nakhala wodzitsutsa yekha.

12 2Tim. 4.12 Pamene ndikatuma Aritema kwa iwe, kapena Tikiko, chita changu kudza kwa ine ku Nikopoli: pakuti ndatsimikiza mtima kugonerako nyengo yachisanu.

13Mac. 18.24Zena nkhoswe ya milandu, ndi Apolo ufulumire kuwakonzera zaulendo, kuti asasowe kanthu,

14Tit. 3.8Ndipo anthu athu aphunzirenso asunge ntchito zabwino zofunika, kuti asakhale osabala zipatso.

15Akukupatsa moni onse akukhala pamodzi ndi ine. Pereka moni kwa otikondawo m'chikhulupiriro. Chisomo chikhale ndi inu nonse.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help