1Pamenepo Elifazi wa ku Temani anayankha, nati,
2Kodi mwini nzeru ayankhe ndi kudziwa kouluzika,
ndi kudzaza mimba yake ndi mphepo ya kum'mawa?
3Kodi atsutsane ndi mnzake ndi mau akusathandiza?
Kapena ndi maneno akusapindulitsa?
4Zedi uyesa chabe mantha,
nuchepsa chilingiriro pamaso pa Mulungu.
5Pakuti pakamwa pako paphunzitsa mphulupulu zako,
nusankha lilime la ochenjerera.
6 Luk. 19.22 Pakamwa pako pakutsutsa, si ine ai.
Inde milomo yako ikuchitira umboni wakukutsutsa.
7Kodi ndiwe munthu woyamba kubadwa?
Kapena unayamba kulengedwa ndiwe, osati mapiri?
8 Aro. 11.34 Kodi unamva uphungu wachinsinsi wa Mulungu?
Ndipo unadzikokera nzeru kodi?
9Udziwa chiyani, osachidziwa ife?
Uzindikira chiyani, chosakhala mwa ife?
10Pakati pa ife pali aimvi, ndi okalambitsa,
akuposa atate wako masiku ao.
11Masangalatso a Mulungu akuchepera kodi?
Kapena uli nacho chinsinsi kodi?
12Mtima wako usonthokeranji nawe?
Maso ako aphethiraphethira chifukwa ninji?
13Kuti utembenuza mzimu wako utsutsane ndi Mulungu,
ndi kulola mau otere atuluke m'kamwa mwako.
14 Mas. 14.3 Munthu nchiyani kuti akhale woyera,
wobadwa ndi mkazi kuti akhale wolungama?
15Taona, Mulungu sakhulupirira opatulika ake;
ngakhale m'mwamba simuyera pamaso pake.
16 Mas. 53.3 Koposa kotani nanga munthu wonyansa ndi wodetsa,
wakumwa chosalungama ngati madzi.
17Ndidzakuonetsa, undimvere;
chimene ndinachiona, ndidzakufotokozera;
18chimene adachinena anzeru,
adachilandira kwa makolo ao, osachibisa;
19ndiwo amene analandira okha dzikoli,
wosapita mlendo pakati pao.
20Munthu woipa adzipweteka masiku ake onse,
ndi zaka zowerengeka zisingikira woopsa.
21 1Ate. 5.3 M'makutu mwake mumveka zoopsetsa;
pali mtendere amfikira wakumuononga.
22Sakhulupirira kuti adzatulukamo mumdima,
koma kuti lupanga limlindira.
23Ayendayenda ndi kufuna chakudya, nati, Chilikuti?
Adziwa kuti lamkonzekeratu pafupi tsiku lamdima.
24Nsautso ndi chipsinjo zimchititsa mantha,
zimgonjetsa ngati mfumu yokonzekeratu kunkhondo.
25Pakuti amtambasula dzanja lake moyambana ndi Mulungu,
napikisana ndi Wamphamvuyonse.
26Amthamangira Iye mwaliuma,
ndi zikopa zake zochindikira.
27Popeza anakuta nkhope yake ndi kunenepa kwake,
nachita mafunyenye a mafuta m'zuuno zake;
28adzakhala m'mizinda yopasuka,
m'nyumba zosakhalamo munthu,
zoti zisandulika muunda.
29Sadzakhala wolemera, ndi chuma chake sichidzakhalitsa,
ndi zipatso zake sizidzachuluka padziko.
30Sadzachoka mumdima;
lawi la moto lidzaumitsa nthambi zake;
ndipo adzachoka ndi mpumo wa m'kamwa mwake.
31 Yes. 59.4 Asatame zopanda pake, kudzinyenga nazo;
pakuti zopanda pake zidzakhala chombwezera chake.
32Chidzachitika isanadze nthawi yake;
pakuti nthambi yake siidzaphuka.
33Adzayoyoka zipatso zake zosapsa ngati mpesa,
nadzathothoka maluwa ake ngati mtengo wa azitona.
34Pakuti msonkhano wa onyoza Mulungu udzakhala chumba,
ndi moto udzapsereza mahema a olandira chokometsera mlandu.
35 Mas. 7.14 Aima ndi chovuta, nabala mphulupulu,
ndi m'mimba mwao mukonzeratu chinyengo.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.