YOBU Mau Oyamba - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Mau OyambaBukuli likukamba za Yobu, munthu wolungama amene anakumana ndi mavuto aakulu, nakhala akuzunzika ndi kudandaula, nafunitsitsa kudziwa chifukwa chimene Mulungu walolera zoterezi.Yobu anagwa m'mavuto aakulu: ana ake onse anafa, chuma chake chonse nkuwonongeka, ndipo mwinawakeyo anagwidwa ndi nthenda yoopsa, thupi lake nkuwola.Abwenzi ake atatu anabwera kudzampepesa pa mavuto akewo, nayamba kukambirana za gwero lake la mavutowo, aliyense natulutsa maganizo ake. Abwenzi atatu aja, pofuna kufotokoza za gwero la mavuto a Yobu, angotsata maganizo a makolo achiyuda, akuti Mulungu amadalitsa anthu abwino ndipo amalanga anthu ochimwa; ndiye kuti mavuto amene Yobuyu anakumana nawo akusonyeza kuti iye anachimwa. Pamenepo Yobu akuti, Iyayi, nchosatheka; pakuti iyeyo wakhala akuyesetsa kukhala wabwino ndi wolungama masiku onse. Chifukwa chosamvetsa gwero lake la mavuto akewo, ayamba kufunsa Mulungu mafunso, ndipo amupempha kuti achitepo kanthu kosonyeza kuti iye ngwolungamadi, ndipo motero mbiri yake isaipitsidwe pamaso pa anthu.Yehova poyankha sasamala mafunso a Yobu aja, angomuwonetsa ukulu wake, mphamvu zake ndi nzeru zake zodabwitsa, kulimbitsa chikhulupiriro cha Yobu. Apo Yobuyo adzichepetsa pamaso pa Mulungu ndipo amupepesa chifukwa cha mau okalipa aja omwe iye adalankhula potsutsana ndi Yehova.Pambuyo pake Mulungu amudalitsa Yobu pomubwezera zabwino zake mowirikiza, ndipo adzudzula abwenzi ake atatu aja, chifukwa iwo adalephera kumvetsa tanthauzo la mavuto a Yobu. Yobu yekhayu adazindikira kuti Mulungu ngwamkulu koposa m'mene makolo achiyuda ankaganizira.Za mkatimuMau oyambirira 1.1—2.13

Yobu ndi abwenzi ake 3.1—31.40

a. Kudandaula kwa Yobu 3.1-26

b. Kukambirana koyamba 4.1—14.22

c. Kukambirana kwachiwiri 15.1—21.34

d. Kukambirana kwachitatu 22.1—27.23

e. Mau oyamikira nzeru 28.1-28

f. Mau otsiriza a Yobu 29.1—31.40

Mau a Elihu 32.1—37.24

Mau a Yehova oyankha Yobu 38.1—42.6

Mau omaliza 42.7-17

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help