1 Mas. 18.48 Ndilanditseni kwa adani anga, Mulungu wanga,
ndiikeni pamsanje kwa iwo akundiukira.
2Mundilanditse kwa ochita zopanda pake,
ndipo ndipulumutseni kwa anthu olira mwazi.
3 1Sam. 24.11 Pakuti onani, alalira moyo wanga;
amphamvu andipangira chiwembu,
osachimwa, osalakwa ine, Yehova,
4osawapatsa chifukwa ine, athamanga nadzikonza.
Galamukani kukomana nane, ndipo penyani.
5Ndinu Yehova, Mulungu wa makamu, Mulungu wa Israele.
Ukani kukazonda amitundu onse,
musachitire chifundo mmodzi yense
wakuchita zopanda pake monyenga.
6Abwera madzulo, auwa ngati galu,
nazungulira mzinda.
7Onani abwetuka pakamwa pao;
m'milomo mwao muli lupanga,
pakuti amati, Amva ndani?
8 Mas. 2.4 Koma Inu, Yehova, mudzawaseka;
mudzalalatira amitundu onse.
9Inu, mphamvu yanga, ndidzakulindirani;
pakuti Mulungu ndiye msanje wanga.
10 Mas. 21.3 Mulungu wa chifundo changa adzandichingamira,
adzandionetsa tsoka la adani anga.
11Musawapheretu, angaiwale anthu anga,
muwabalalitse mwa mphamvu yanu, ndipo muwagwetse,
Ambuye, ndinu chikopa chathu.
12 Miy. 12.13 Pakamwa pao achimwa ndi mau onse a pa milomo yao,
potero akodwe m'kudzitamandira kwao,
ndiponso chifukwa cha kutemberera ndi bodza azilankhula.
13 Mas. 83.18 Muwathe mumkwiyo, muwagulule psiti.
Ndipo adziwe kuti Mulungu ndiye woweruza mu Yakobo,
kufikira malekezero a dziko la pansi.
14 Mas. 59.6 Ndipo abwere madzulo, auwe ngati galu,
nazungulire mzinda.
15Ayendeyende ndi kufuna chakudya,
nachezere osakhuta.
16Koma ine, ndidzaimbira mphamvu yanu;
inde ndidzaimbitsa chifundo chanu mamawa,
pakuti Inu mwakhala msanje wanga,
ndi pothawirapo ine tsiku la nsautso yanga.
17 Mas. 18.1-2 Ndidzaimbira zakukulemekezani Inu, mphamvu yanga;
pakuti Mulungu ndiye msanje wanga,
Mulungu wa chifundo changa.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.