1 Mac. 18.27 Kodi tilikuyambanso kudzivomereza tokha? Kapena kodi tisowa, monga ena, makalata otivomerezetsa kwa inu, kapena ochokera kwa inu?
21Ako. 9.2Inu ndinu kalata yathu, wolembedwa mu mitima yathu, wodziwika ndi wowerengedwa ndi anthu onse;
3Eks. 24.12; Yer. 31.33popeza mwaonetsedwa kuti muli kalata ya Khristu, wakumtumikira ndi ife, wosalembedwa ndi kapezi iai, koma ndi Mzimu wa Mulungu wamoyo; wosati m'magome amiyala, koma m'magome a mitima yathupi.
4Ndipo kulimbika kotere kwa Mulungu tili nako mwa Khristu:
5Yoh. 15.5; 1Ako. 15.10; 2Ako. 2.16si kuti tili okwanira pa ife tokha, kuyesera kanthu monga mochokera mwa ife tokha; kukwanira kwathu kuchokera kwa Mulungu;
6Yer. 31.31, 33; Yoh. 6.63; Aro. 8.2; Aef. 3.7amenenso anatikwaniritsa ife tikhale atumiki a pangano latsopano; si la chilembo, koma la mzimu; pakuti chilembo chipha, koma mzimu uchititsa moyo.
7Eks. 34.29-30, 35Koma ngati utumiki wa imfa wolembedwa ndi wolochedwa m'miyala, unakhala mu ulemerero, kotero kuti ana a Israele sanathe kuyang'anitsa pa nkhope yake ya Mose, chifukwa cha ulemerero wa nkhope yake, umene unalikuchotsedwa:
8koposa kotani nanga utumiki wa Mzimu udzakhala mu ulemerero?
9Aro. 3.21Pakuti ngati utumiki wa chitsutso unali wa ulemerero, makamaka utumiki wa chilungamo uchulukira muulemerero kwambiri.
10Pakutinso chimene chinachitidwa cha ulemerero sichinachitidwe cha ulemerero m'menemo, chifukwa cha ulemerero woposawo.
11Pakuti ngati chimene chilikuchotsedwa chinakhala mu ulemerero, makamaka kwambiri chotsalacho chili mu ulemerero.
12Pokhala nacho tsono chiyembekezo chotere, tilankhula ndi kukhazikika mtima kwakukulu,
13Eks. 34.29-30, 35ndipo si monga Mose, amene anaika chophimba pa nkhope yake, kuti ana a Israele asayang'anitse pa chimaliziro cha chimene chinalikuchotsedwa;
14Yes. 6.10; Aro. 11.7-8, 25koma mitima yao inaumitsidwa; pakuti kufikira lero lomwe lino, pa kuwerenga kwa pangano lakale chophimba chomwechi chikhalabe chosavundukuka, chimene chilikuchotsedwa mwa Khristu.
15Koma kufikira lero, pamene awerengedwa Mose, chophimba chigona pamtima pao.
16Aro. 11.23, 26Koma pamene akatembenukira kwa Ambuye, chophimbacho chichotsedwa.
17Koma Ambuye ndiye Mzimuyo; ndipo pamene pali Mzimu wa Ambuye pali ufulu.
18Aro. 8.29; 1Ako. 15.49Koma ife tonse ndi nkhope yosaphimbika popenyerera monga mwa kalirole ulemerero wa Ambuye, tisandulika m'chithunzithunzi chomwechi kuchokera kuulemerero kunka kuulemerero, monga ngati kuchokera kwa Ambuye Mzimu.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.