1 Mas. 135.1 Aleluya;
Lemekezani, inu atumiki a Yehova;
lemekezani dzina la Yehova.
2Lodala dzina la Yehova Kuyambira tsopano kufikira kosatha.
3 Yes. 59.19 Chitulukire dzuwa kufikira kulowa kwake
lilemekezedwe dzina la Yehova.
4Yehova akwezeka pamwamba pa amitundu onse,
ulemerero wake pamwambamwamba.
5 Mas. 89.6 Akunga Yehova Mulungu wathu ndani?
Amene akhala pamwamba patali,
6 Yes. 57.15 nadzichepetsa apenye
zam'mwamba ndi za padziko lapansi.
7 1Sam. 2.8 Amene autsa wosauka kumchotsa kufumbi,
nakweza waumphawi kumchotsa kudzala.
8Kuti amkhalitse pamodzi ndi akulu,
pamodzi ndi akulu a anthu ake.
9 1Sam. 2.5; Yes. 54.1; Agal. 4.27 Asungitsa nyumba mkazi wosaona mwana,
akhale mai wokondwera ndi ana.
Aleluya.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.