1 2Ako. 13.13 Ngati tsono muli chitonthozo mwa Khristu, ngati chikhazikitso cha chikondi, ngati chiyanjano cha Mzimu, ngati phamphu, ndi zisoni,
21Pet. 3.8kwaniritsani chimwemwe changa, kuti mukalingalire mtima zomwezo, akukhala nacho chikondi chomwe, a moyo umodzi, olingalira mtima umodzi;
3Yak. 3.4; 1Pet. 5.5musachite kanthu monga mwa chotetana, kapena monga mwa ulemerero wopanda pake, komatu ndi kudzichepetsa mtima, yense ayese anzake omposa iye mwini;
41Ako. 10.24, 33munthu yense asapenyerere zake za iye yekha, koma yense apenyererenso za mnzake.
5Yoh. 13.15Mukhale nao mtima m'kati mwanu umene unalinso mwa Khristu Yesu,
6Yoh. 1.1-2ameneyo, pokhala nao maonekedwe a Mulungu, sanachiyese cholanda kukhala wofana ndi Mulungu,
7Mas. 22.6; Yes. 53.3, 11; Luk. 22.27; Yoh. 1.14koma anadzikhuthula yekha, natenga maonekedwe a kapolo, nakhala m'mafanizidwe a anthu;
8Mat. 26.42ndipo popezedwa m'maonekedwe ngati munthu, anadzichepetsa yekha, nakhala womvera kufikira imfa, ndiyo imfa ya pamtanda.
9Aef. 1.20-21Mwa ichinso Mulungu anamkwezetsa Iye, nampatsa dzina limene liposa maina onse,
10Aro. 14.11kuti m'dzina la Yesu bondo lililonse lipinde, la za m'mwamba ndi za padziko, ndi za pansi padziko,
11Mac. 2.36ndi malilime onse avomere kuti Yesu Khristu ali Ambuye, kuchitira ulemu Mulungu Atate.
12Potero, okondedwa anga, monga momwe mumvera nthawi zonse, posati pokhapokha pokhala ine ndilipo, komatu makamaka tsopano pokhala ine palibe, gwirani ntchito yake ya chipulumutso chanu ndi mantha, ndi kunthunthumira;
13Aheb. 13.21pakuti wakuchita mwa inu kufuna ndi kuchita komwe, chifukwa cha kukoma mtima kwake, ndiye Mulungu.
141Pet. 4.9Chitani zonse kopanda madandaulo ndi makani,
15Mat. 5.14, 16kuti mukakhale osalakwa ndi oona, ana a Mulungu opanda chilema pakati pa mbadwo wokhotakhota ndi wopotoka, mwa iwo amene muonekera monga mauniko m'dziko lapansi,
161Ate. 2.19akuonetsera mau a moyo; kuti ine ndikakhale wakudzitamandira nao m'tsiku la Khristu, kuti sindinathamange chabe, kapena kugwiritsa ntchito chabe.
172Tim. 4.6Komatu ngatinso ndithiridwa pa nsembe ndi kutumikira kwa chikhulupiriro chanu, ndikondwera, ndipo ndikondwera pamodzi ndi inu nonse;
18momwemonso kondwerani inu, nimukondwere pamodzi ndi ine.
Paulo atamula Timoteo ndi Epafrodito amithenga ake a kwa Afilipi19 1Ate. 3.2 Koma ndiyembekeza mwa Ambuye Yesu kuti ndidzatumiza Timoteo kwa inu msanga, kuti inenso nditonthozeke bwino pozindikira za kwa inu.
20Pakuti ndilibe wina wa mtima womwewo, amene adzasamalira za kwa inu ndi mtima woona.
212Tim. 4.10, 16Pakuti onsewa atsata za iwo okha, si za Yesu Khristu.
221Tim. 1.2Koma muzindikira matsimikizidwe ake, kuti, monga mwana achitira atate wake, anatumikira pamodzi ndi ine Uthenga Wabwino.
23Ameneyo ndithu tsono ndiyembekeza kumtuma posachedwa m'mene ndikapenyerera za kwa ine zidzatani;
24Afi. 1.25koma ndikhulupirira mwa Ambuye kuti ine ndekhanso ndidzadza msanga.
25Afi. 4.18Koma ndinayesa nkofunika kutuma kwa inu Epafrodito mbaleyo, ndiye wantchito mnzanga ndi msilikali mnzanga, ndiye mtumwi wanu, ndi wonditumikira pa chosowa changa;
26popeza anali wolakalaka inu nonse, navutika mtima chifukwa mudamva kuti anadwala.
27Pakutinso anadwaladi pafupi imfa; komatu Mulungu anamchitira chifundo; koma si iye yekha, komatu inenso, kuti ndisakhale nacho chisoni chionjezereonjezere.
28Chifukwa chake ndamtuma iye chifulumizire, kuti pakumuona mukakondwerenso, ndi inenso chindichepere chisoni.
291Tim. 5.17Chifukwa chake mumlandire mwa Ambuye, ndi chimwemwe chonse; nimuchitire ulemu oterewa;
30Afi. 4.10pakuti chifukwa cha ntchito ya Khristu anafikira pafupi imfa, wosasamalira moyo wake, kuti akakwaniritse chiperewero cha utumiki wanu wa kwa ine.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.