MIYAMBO 2 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Ukoma ndi phindu lake la Nzeru

1 Miy. 4.21 Mwananga, ukalandira mau anga,

ndi kusunga malamulo anga;

2kutcherera makutu ako kunzeru,

kulozetsa mtima wako kukuzindikira;

3ukaitananso luntha,

ndi kufuulira kuti ukazindikire;

4 Mat. 13.44 ukaifunafuna ngati siliva,

ndi kuipwaira ngati chuma chobisika;

5pompo udzazindikira kuopa Yehova

ndi kumdziwadi Mulungu.

6 1Maf. 3.9, 12; Yak. 1.5 Pakuti Yehova apatsa nzeru;

kudziwa ndi kuzindikira kutuluka m'kamwa mwake.

7Iye asungira oongoka mtima nzeru yeniyeni;

ndiye chikopa cha oyenda molunjika;

8 1Sam. 2.9 kuti atchinjirize njira za chiweruzo,

nadikire khwalala la opatulidwa ake.

9Pamenepo udzazindikira chilungamo ndi chiweruzo,

zolunjika ndi mayendedwe onse abwino.

10Pakuti nzeru idzalowa m'mtima mwako,

moyo wako udzakondwera ndi kudziwa,

11kulingalira kudzakudikira,

kuzindikira kudzakutchinjiriza;

12kukupulumutsa kunjira yoipa,

kwa anthu onena zokhota;

13 Yoh. 3.19-20 akusiya mayendedwe olungama,

akayende m'njira za mdima;

14 Aro. 1.32 omwe asangalala pochita zoipa,

nakondwera ndi zokhota zoipa;

15amene apotoza njira zao,

nakhotetsa mayendedwe ao.

16 Miy. 5.3, 20 Nzeru idzakupulumutsa kwa mkazi wachiwerewere,

kwa mkazi wachilendo wosyasyalika ndi mau ake;

17wosiya bwenzi la ubwana wake,

naiwala chipangano cha Mulungu wake.

18 Miy. 7.27 Nyumba yake itsikira kuimfa,

ndi mayendedwe ake kwa akufa;

19onse akunka kwa iye sabweranso,

safika kunjira za moyo;

20nzeru idzakuyendetsa m'njira ya anthu abwino,

kuti usunge mayendedwe a olungama.

21 Mas. 37.28-29 Pakuti oongoka mtima adzakhala m'dziko,

angwiro nadzatsalamo.

22Koma oipa adzalikhidwa m'dziko,

achiwembu adzazulidwamo.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help