1 Mas. 118.5; Yon. 2.2 Ndinafuulira kwa Yehova mu msauko wanga,
ndipo anandivomereza.
2Yehova, landitsani moyo wanga kumilomo ya mabodza,
ndi kulilime lonyenga.
3Adzakuninkhanji, adzakuonjezeranji,
lilime lonyenga iwe?
4Mivi yakuthwa ya chiphona,
ndi makala tsanya.
5 Gen. 25.13; Ezk. 27.13 Tsoka ine, kuti ndili mlendo mu Meseki,
kuti ndigonera m'mahema a Kedara!
6Moyo wanga unakhalitsa nthawi
pamodzi ndi iye wakudana nao mtendere.
7Ine ndikuti, Mtendere;
koma polankhula ine, iwowa akuti, Nkhondo.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.