1Ndipo awa ndi malamulo, malemba, ndi maweruzo, amene Yehova Mulungu wanu analamulira kukuphunzitsani, kuti muziwachita m'dziko limene muolokerako kulilandira;
2kuti muope Yehova Mulungu wanu, kusunga malemba ake onse ndi malamulo ake, amene ndikuuzani inu ndi ana anu, ndi zidzukulu zanu, masiku onse a moyo wanu, ndi kuti masiku anu achuluke.
3Eks. 3.8Potero imvani, Israele, musamalire kuwachita, kuti chikukomereni ndi kuti muchuluke chichulukire, monga Yehova Mulungu wa makolo anu anena ndi inu, m'dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi.
4 Mrk. 12.29-30 Imvani, Israele; Yehova Mulungu wathu, Yehova ndiye mmodzi;
5ndipo muzikonda Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse, ndi mphamvu yanu yonse.
6Ndipo mau awa ndikuuzani lero, azikhala pamtima panu;
7Deut. 4.9ndipo muziwaphunzitsa mwachangu kwa ana anu, ndi kuwalankhula awa pokhala pansi m'nyumba zanu, ndi poyenda inu panjira, ndi pogona inu pansi, ndi pouka inu.
8Deut. 11.18; Miy. 6.21Ndipo muziwamanga padzanja panu ngati chizindikiro, ndipo akhale ngati chapamphumi pakati pamaso anu.
9Ndipo muziwalembera pa mphuthu za nyumba zanu, ndi pa zipata zanu.
10Ndipo kudzakhala, Yehova Mulungu wanu atakulowetsani m'dziko limene analumbirira makolo anu, Abrahamu, Isaki, ndi Yakobo, kuti adzakupatsani ili; mizinda yaikulu ndi yokoma, imene simunaimange;
11ndi nyumba zodzala nazo zokoma zilizonse, zimene simunazidzaze, ndi zitsime zosema, zimene simunaziseme, minda yampesa, ndi minda ya azitona, zimene simunazioke, ndipo mutakadya ndi kukhuta;
12pamenepo mudzichenjera mungaiwale Yehova, amene anakutulutsani m'dziko la Ejipito, m'nyumba ya ukapolo.
13Luk. 4.8Muziopa Yehova Mulungu wanu; ndi kutumikira Iyeyu; ndipo polumbira muzitchula dzina lake.
14Yer. 25.6Musamatsate milungu ina, milungu ina ya mitundu ya anthu akuzinga inu;
15pakuti Yehova Mulungu wanu ali pakati panu, ndiye Mulungu wansanje; kuti ungapse mtima wa Yehova Mulungu wanu, ndi kukuonongani, kukuchotsani pankhope padziko lapansi.
16 Mat. 4.7 Musamayesa Yehova Mulungu wanu, monga munamyesa mu Masa.
17Muzisunga mwachangu malamulo a Yehova Mulungu wanu, ndi mboni zake, ndi malemba ake, amene anakulamulirani.
18Ndipo muzichita zolunjika ndi zokoma pamaso pa Yehova; kuti chikukomereni, ndi kuti mulowe kukalandira dziko lokomali Yehova analumbirira makolo anu,
19kuingitsa adani anu onse pamaso panu, monga Yehova adanena.
20 Eks. 13.14 Akakufunsani ana anu m'tsogolomo, ndi kuti, Mbonizo, ndi malemba, ndi maweruzo, zimene Yehova Mulungu wathu anakulamulirani, zitani?
21Pamenepo muzinena kwa ana anu, Tinali akapolo a Farao mu Ejipito; ndipo Yehova anatitulutsa mu Ejipito ndi dzanja lamphamvu.
22Eks. 7.8Ndipo Yehova anapatsa zizindikiro ndi zozizwa zazikulu ndi zowawa mu Ejipito, pa Farao, ndi pa nyumba yake yonse, pamaso pathu;
23ndipo anatitulutsa komweko, kuti atilowetse, kutipatsa dzikoli analumbirira makolo athu.
24Yer. 32.39Ndipo Yehova anatilamulira tizichita malemba awa onse, kuopa Yehova Mulungu wathu, kuti tipindule nako masiku onse, kuti atisunge amoyo, monga lero lino.
25Ndipo kudzakhala kwa ife chilungamo, ngati tisamalira kuchita malamulo awa onse pamaso pa Yehova Mulungu wathu, monga anatilamulira ife.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.