1Awa ndi malemba ndi maweruzo, muziwasamalirawa kuwachita m'dziko limene Yehova Mulungu wa makolo anu anakupatsani likhale lanulanu, masiku onse akukhala ndi moyo inu padziko lapansi.
2Eks. 34.13Muononge konse malo onse, amitundu amene mudzawalanda anatumikirako milungu yao, pa mapiri aatali, ndi pa zitunda, ndi pansi pa mitengo yonse yabiriwiri;
3Ower. 2.2nimugumule maguwa ao a nsembe, ndi kuphwanya zoimiritsa zao, ndi kutentha zifanizo zao, ndi kulikha mafano osema a milungu yao; ndipo muononge dzina lao lichoke m'malomo.
4Musamatero ndi Yehova Mulungu wanu.
51Maf. 8.29; 2Mbi. 7.12Koma kumalo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha mwa mafuko anu onse kuikapo dzina lake, ndiko ku chokhalamo chake, muzifunako, ndi kufikako;
6ndi kubwera nazo kumeneko nsembe zanu zopsereza, ndi nsembe zanu zophera, ndi magawo anu onse a magawo khumi, ndi nsembe yokweza ya dzanja lanu, ndi zowinda zanu, ndi nsembe zanu zaufulu, ndi zoyamba kubadwa za ng'ombe zanu, ndi za nkhosa ndi mbuzi zanu;
7ndipo kumeneko muzidya pamaso pa Yehova Mulungu wanu, ndi kukondwera nazo zonse mudazigwira ndi dzanja lanu, inu ndi a pa banja lanu, m'mene Yehova Mulungu wanu anakudalitsani.
8Musamadzichita monga mwa zonse tizichita kuno lero, yense kuchita chilichonse chiyenera m'maso mwake;
9pakuti mpaka lero simunafikire mpumulo ndi cholowa, zimene Yehova Mulungu wanu adzakupatsani.
10Koma mudzaoloka Yordani, ndi kukhala m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akulandiritsani; ndipo adzakupumulitsani akulekeni adani anu onse pozungulirapo, ndipo mudzakhala mokhazikika.
11Deut. 12.5Pamenepo padzakhala malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha kukhalitsako dzina lake, kumeneko muzibwera nazo zonse ndikuuzanizi; nsembe zanu zopsereza, ndi nsembe zanu zophera, magawo anu onse a magawo khumi, ndi nsembe yokweza dzanja lanu, ndi zowinda zanu zosankhika zimene muzilonjezera Yehova.
12Ndipo mudzakondwera pamaso pa Yehova Mulungu wanu, inu ndi ana anu aamuna, ndi ana anu aakazi, ndi antchito anu aamuna, ndi antchito anu aakazi, ndi Mlevi ali m'midzi mwanu, popeza alibe gawo kapena cholowa pamodzi ndi inu.
13Dzichenjerani nokha, musamapereka nsembe zanu zopsereza pamalo ponse upaona:
14koma pamalo pamene Yehova adzasankha, mwa limodzi la mafuko anu, pamenepo muzipereka nsembe zanu zopsereza, ndi pamenepo muzichita zonse ndikuuzani.
15Koma monga mwa chikhumbo chonse cha moyo wanu muiphe ndi kudya nyama m'midzi yanu yonse, monga mwa mdalitso wa Yehova Mulungu wanu anakupatsani; odetsa ndi oyera adyeko, monga yamphoyo ndi yangondo.
16Gen. 9.4Mwazi wao wokha musamadya; muziuthira panthaka ngati madzi.
17Simungathe kudya m'mudzi mwanu limodzi la magawo khumi la tirigu wanu, kapena la vinyo wanu, kapena la mafuta anu, kapena oyamba kubadwa a ng'ombe zanu kapena la nkhosa ndi mbuzi zanu, kapena zowinda zanu zilizonse muzilonjeza kapena nsembe zanu zaufulu, kapena nsembe yokweza ya m'dzanja lanu;
18koma muzizidya pamaso pa Yehova Mulungu wanu m'malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha, inu, ndi ana anu aamuna, ndi ana anu aakazi, ndi antchito anu aamuna, ndi antchito anu aakazi, ndi Mlevi ali m'mudzi mwanu; nimukondwere pamaso pa Yehova Mulungu wanu m'zonse mudazigwira ndi dzanja lanu.
19Deut. 14.27Dzichenjerani nokha, musataye Mlevi masiku onse akukhala inu m'dziko mwanu.
Za kudya nyama20Akadzakuza malire a dziko lanu Yehova Mulungu wanu, monga ananena ndi inu, ndipo mukadzati, Ndidye nyama, popeza moyo wanga ukhumba kudya nyama; mudye nyama monga umo monse ukhumba moyo wanu.
21Malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha kuikako dzina lake akakutanimphirani, muziphako ng'ombe zanu ndi nkhosa ndi mbuzi zanu zimene Yehova anakupatsani, monga ndinakuuzani, ndi kuzidya m'mudzi mwanu, monga umo monse ukhumba moyo wanu.
22Koma monga umo amadya mphoyo ndi ngondo momwemo uzizidya; odetsa ndi oyera adyeko chimodzimodzi.
23Koma mulimbikepo ndi kusadya mwaziwo; popeza mwazi ndiwo moyo, nimusamadya moyo pamodzi ndi nyama yake.
24Musamadya uwu; muuthire pansi ngati madzi.
251Maf. 11.38; Yes. 3.10Musamadya uwu; kuti chikukomereni inu, ndi ana anu akudza m'mbuyo mwanu, pakuchita inu zoyenera pamaso pa Yehova.
26Zopatulika zanu zokha zimene muli nazo, ndi zowinda zanu, muzitenge, ndi kupita nazo ku malo amene Yehova adzasankha;
27ndipo mupereke nsembe zanu zopsereza, nyama zao ndi mwazi wao, paguwa la nsembe la Yehova Mulungu wanu; ndipo athire mwazi wa nsembe zanu zophera paguwa la nsembe la Yehova Mulungu wanu, koma nyama yake muidye.
28Deut. 12.25Samalirani ndi kumvera mau awa onse ndikuuzaniwa, kuti chikukomereni inu, ndi ana anu akudza m'mbuyo mwanu nthawi zonse, pochita inu zokoma ndi zoyenera pamaso pa Yehova Mulungu wanu.
29Pamene Yehova Mulungu wanu akadzadulatu amitundu pamaso panu, kumene mulowako kuwalandira, ndipo mutawalandira, ndi kukhala m'dziko lao,
30Deut. 7.16dzichenjerani nokha mungakodwe ndi kuwatsata, ataonongeka pamaso panu; ndi kuti mungafunsire milungu yao, ndi kuti, Amitundu awa atumikira milungu yao bwanji? Ndichite momwemo inenso.
31Musamatero ndi Yehova Mulungu wanu; pakuti zilizonse zinyansira Yehova, zimene azida Iye, iwowa anazichitira milungu yao; pakuti angakhale ana ao aamuna ndi ana ao aakazi awatentha m'moto, nsembe ya milungu yao.
32Deut. 4.2Chilichonse ndikuuzani, muchisamalire kuchichita; musamaonjezako, kapena kuchepsako.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.