YOBU 33 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Elihu atsutsa Yobu pa kudzikuza kwake, nanenetsa kuti pomlanga munthu Mulungu ali nacho chifukwa

1Komatu, Yobu, mumvere maneno anga,

mutcherere khutu mau anga.

2Taonani tsono, ndatsegula pakamwa panga,

lilime langa lanena m'kamwa mwanga.

3Maneno anga awulula chiongoko cha mtima wanga,

ndi monga umo idziwira milomo yanga idzanena zoona.

4 Gen. 2.7 Mzimu wa Mulungu unandilenga,

ndi mpweya wa Wamphamvuyonse umandipatsa moyo.

5Ngati mukhoza, mundiyankhe;

mulongosolere mau anu pamaso panga, mukonzeke.

6Taonani, ndikhala kwa Mulungu ngati inu;

inenso ndinaumbidwa ndi dothi.

7Taonani, kuopsa kwanga simudzachita nako mantha;

ndi ichi ndikusenzetsani sichidzakulemererani.

8Zedi mwanena m'makutu mwanga,

ndinamvanso mau a kunena kwanu, akuti,

9 Yob. 10.7 Ndine woyera ine, wopanda kulakwa,

ndine wosapalamula, ndilibe mphulupulu.

10Taonani, Iye apeza zifukwa zoti anditsutse nazo,

andiyesa mdani wake;

11amanga mapazi anga m'zigologolo,

ayang'anira poyenda ine ponse.

12Taonani, ndidzakuyankhani m'mene muli mosalungama;

pakuti Mulungu ndiye wamkulu woposa munthu.

13 Yes. 45.9 Mutsutsana ndi Iye chifukwa ninji?

Popeza pa zake zonse sawulula chifukwa.

14Pakuti Mulungu alankhula kamodzi,

kapena kawiri, koma anthu sasamalira.

15 Num. 12.6 M'kulota, m'masomphenya a usiku,

pakuwagwera anthu tulo tatikulu,

pogona mwatcheru pakama,

16pamenepo atsegula makutu a anthu,

nakomera chizindikiro chilangizo chao;

17kuti achotse munthu ku chimene akadachita,

ndi kubisira munthu kudzikuza kwake;

18kuti amletse angaonongeke,

ndi moyo wake ungatayike ndi lupanga.

19Alangidwanso ndi zowawa pakama pake,

ndi kulimbana kowawa kosapuma m'mafupa ake.

20M'mwemo mtima wake uchita mseru ndi mkate,

ndi moyo wake pa chakudya cholongosoka.

21Mnofu wake udatha, kuti sungapenyeke;

ndi mafupa ake akusaoneka atuluka.

22Inde wasendera kufupi kumanda,

ndi moyo wake kwa akuononga.

23Akakhala kwa iye mthenga,

womasulira mau mmodzi mwa chikwi,

kuonetsera munthu chomuyenera;

24pamenepo Mulungu amchitira chifundo, nati,

Mlanditse, angatsikire kumanda, Ndampezera dipo.

25Mnofu wake udzakhala see, woposa wa mwana;

adzabwerera kumasiku a ubwana wake.

26Apembedza Mulungu, ndipo amkomera mtima;

m'mwemo aona nkhope yake mokondwera;

ndipo ambwezera munthu chilungamo chake.

27 2Sam. 12.13; Miy. 28.13; Luk. 15.21; 1Yoh. 1.9 Apenyerera anthu, ndi kuti,

ndinachimwa, ndaipsa choongokacho,

ndipo sindinapindule nako.

28 Yes. 38.17 Koma anandiombola ndingatsikire kumanda,

ndi moyo wanga udzaona kuunika.

29Taona, izi zonse azichita Mulungu

kawiri katatu ndi munthu,

30kumbweza angalowe kumanda,

kuti kuunika kwa moyo kumuwalire.

31Tcherani khutu, Yobu, mundimvere ine;

mukhale chete, ndipo ndidzanena ine.

32Ngati muli nao mau mundiyankhe.

Nenani, pakuti ndifuna kukulungamitsani.

33Ngati mulibe mau, tamverani ine;

mukhale chete, ndipo ndidzakuphunzitsani nzeru.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help