NYIMBO YA SOLOMONI 1 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Mkwatibwi anena ndi ana a Yerusalemu za mkwati

1 1Maf. 4.32 Nyimbo yoposa, ndiyo ya Solomoni.

2Mnyamatayo andipsompsonetse ndi m'kamwa mwake;

pakuti chikondi chako chiposa vinyo.

3Mafuta ako anunkhira bwino;

dzina lako likunga mafuta onunkhira otsanulidwa;

chifukwa chake anamwali akukonda.

4 Hos. 11.4; Aef. 2.6 Undikoke; tikuthamangire;

mfumu yandilowetsa m'zipinda zake:

Tidzasangalala ndi kukondwera ndi iwe.

Tidzatchula chikondi chako koposa vinyo:

Akukonda molungama.

5Wakuda ine, koma wokongola,

ana aakazinu a ku Yerusalemu,

ngati mahema a Kedara,

ngati nsalu zotchinga za Solomoni.

6Musayang'ane pa ine, pakuti ndada,

pakuti dzuwa landidetsa.

Ana aamuna a amai anandikwiyira,

anandisungitsa minda yamipesa;

koma munda wangawanga wamipesa sindinausunge.

7Ndiuze, iwe amene moyo wanga ukukonda,

umaweta kuti gulu lako?

Umaligonetsa kuti pakati pa usana?

Pakuti ndikhalirenji ngati wosochera

pambali pa magulu a anzako?

8Ngati sudziwa, mkaziwe woposa kukongola,

dzituluka kukalondola bande la gululo,

nukawete anaambuzi zako pambali pa mahema a abusa.

Mkwati ndi mkwatibwi akambirana za chikondano chao

9 2Mbi. 1.16-17 Ndakulinganiza, wokondedwa wanga mnyamatawe,

ngati akavalo a magaleta a Farao.

10 Ezk. 16.11-13 Masaya ako akongola ndi nkhata zatsitsi,

ndi khosi lako ndi zinganga za mkanda wonyezimira.

11Tidzakupangira nkhata zagolide

ndi njumu zasiliva.

12Pokhala mfumu podyera pake,

narido wanga ananunkhira.

13Wokondedwa wanga mnyamatayo

ali kwa ine ngati thumba la mure,

logona pakati pa mawere anga.

14Wokondedwa wanga ali kwa ine

ngati chipukutu cha maluwa ofiira

m'minda yamipesa ya ku Engedi.

15Taona, wakongolatu, bwenzi langa;

namwaliwe taona, wakongola,

maso ako akunga a nkhunda.

16Taona, wakongolatu, bwenzi langa,

mnyamatawe, inde, wakongoletsa;

pogona pathu mpa msipu.

17Mitanda ya nyumba zathu nja mikungudza,

ndi mapaso athu nga mlombwa.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help