EZEKIELE 30 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Ejipito adzagonjetsedwa ndi mfumu ya ku Babiloni

1Anandidzeranso mau a Yehova, akuti,

2Wobadwa ndi munthu iwe, nenera, uziti, Atero Ambuye Yehova, Liritsani, Ha, tsikulo!

3Yow. 2.1; Zef. 1.7Pakuti layandikira tsiku, layandikira tsiku la Yehova, tsiku lamitambo, ndiyo nyengo ya amitundu.

4Ezk. 29.19Ndi lupanga lidzadzera Ejipito, ndi mu Kusi mudzakhala kuwawa kwakukulu, pakugwa ophedwa mu Ejipito; ndipo adzachotsa aunyinji ake, ndi maziko ake adzagadamuka.

5Kusi, ndi Puti, ndi Ludi, ndi osokonezeka onse, ndi Libiya, ndi anthu a dziko lopangana nao, adzagwa pamodzi nao ndi lupanga.

6Atero Yehova, Iwonso ochirikiza Ejipito adzagwa, ndi mphamvu yake yodzikuza idzatsika, kuyambira ku Migidoli mpaka ku nsanja ya Siyene adzagwa m'kati mwake ndi lupanga, ati Ambuye Yehova.

7Ndipo adzakhala opasuka pakati pa maiko opasuka, ndi mizinda yake idzakhala pakati pa mizinda yopasuka.

8Ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, nditaika moto mu Ejipito, naonongeka onse akumthandiza.

9Tsiku ilo mithenga idzatuluka pamaso panga m'zombo kuopsa Akusi osalabadira; ndipo kudzakhala kuwawa kwakukulu pakati pao, monga tsiku la Ejipito, pakuti taona, likudza.

10 Ezk. 29.19 Atero Ambuye Yehova, Ndidzaleketsa kusokosera kwa Ejipito ndi dzanja la Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni.

11Ezk. 30.10; 28.7Iye ndi anthu ake pamodzi naye, woopsa amitundu, adzatengedwa aliononge dzikolo, nadzasololera Ejipito malupanga ao, ndi kudzaza dziko ndi ophedwa.

12Yes. 19.5-6Ndipo ndidzaphwetsa mitsinje, ndi kugulira dziko m'dzanja la anthu oipa, ndipo ndidzalisandutsa likhale dziko lopasuka, ndi zonse zili m'mwemo mwa dzanja la alendo; Ine Yehova ndachinena.

13 Yes. 19.1 Atero Ambuye Yehova, Ndidzaononganso mafano, ndi kuleketsa milungu yopanda pake ku Nofu; ndipo sadzaonekanso kalonga wochokera ku Ejipito, ndipo ndidzaopsa dziko la Ejipito.

14Mas. 78.12; Ezk. 29.14Ndipo ndidzasandutsa Patirosi labwinja, ndi kuika moto mu Zowani, ndi kukwaniritsa maweruzo mu No.

15Yer. 46.25Ndipo ndidzatsanulira ukali wanga pa Sini, polimbika penipeni pa Ejipito, ndi kulikha aunyinji a No.

16Ndipo ndidzaika moto mu Ejipito; Sini adzamva kuwawa kwakukulu, ndi No adzagawika pakati, ndi Nofu adzaona adani usana.

17Anyamata a Oni ndi Pibeseti adzagwa ndi lupanga, ndi midziyi idzalowa undende.

18Ndi ku Tehafinehesi kudzada usana, pakuthyola Ine magoli a Ejipito komweko; ndi mphamvu yake yodzikuza idzalekeka m'menemo; kunena za ilo mtambo udzaliphimba, ndi ana ake aakazi adzalowa undende.

19Motero ndidzakwaniritsa maweruzo mu Ejipito, ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

20Ndipo kunali chaka chakhumi ndi chimodzi, mwezi woyamba, tsiku lachisanu ndi chiwiri la mwezi, anandidzera mau a Yehova, akuti,

21Wobadwa ndi munthu iwe, ndathyola dzanja la Farao mfumu ya Aejipito, ndipo taona, silinamangidwe kuti lipole, kulikulunga ndi nsalu, kulilimbitsa ligwire lupanga.

22Mas. 37.17Chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Taona, Ine ndilimbana naye Farao mfumu ya Aejipito, ndidzathyola manja ake, lolimba ndi lothyokalo, ndi kutayitsa lupanga m'dzanja lake.

23Ndipo ndidzamwaza Aejipito mwa amitundu, ndi kuwabalalitsa m'maiko.

24Ndipo ndidzalimbitsa manja a mfumu ya ku Babiloni, ndi kuika lupanga langa m'dzanja lake; koma ndidzathyola manja a Farao, ndipo adzabuula pamaso pake mabuulo a munthu wopyozedwa.

25Mas. 9.16Ndipo ndidzalimbitsa manja a mfumu ya ku Babiloni, koma manja a Farao adzagwa; ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova pakuika Ine lupanga langa m'dzanja la mfumu ya ku Babiloni, nalitambasula iye padziko la Ejipito.

26Ezk. 29.12; 30.23Ndipo ndidzamwaza Aejipito mwa amitundu, ndi kuwabalalitsa mwa amitundu; motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help