1Ndipo anandidzera mau a Yehova, akuti,
2Yer. 31.29Mutani inu ndi kunena mwambi uwu za dziko la Israele, wakuti, Atate adadya mphesa zosacha, ndi mano a ana ayayamira.
3Pali Ine, ati Ambuye Yehova, simudzaonanso chifukwa cha kunena mwambiwu mu Israele.
4Aro. 6.23Taonani, miyoyo yonse ndi yanga, monga moyo wa atate momwemonso moyo wa mwana, ndiyo yanga; moyo wochimwawo ndiwo udzafa.
5Koma munthu akakhala wolungama, nakachita chiweruzo ndi chilungamo,
6wosadya pamapiripo, wosakweza maso ake kumafano a nyumba ya Israele, wosaipsa mkazi wa mnansi wake, kapena kuyandikira mkazi ataoloka,
7Eks. 22.21-26; Deut. 15.7-8; Mat. 25.35-36wosasautsa munthu aliyense, koma wambwezera wangongole chigwiriro chake, wosatenga zofunkha, anampatsa wanjala chakudya chake, naveka wamaliseche ndi chovala,
8Eks. 22.25; Deut. 1.16; Neh. 5.7; Mas. 15.5wosapereka molira phindu, wosatenga choonjezerapo wobweza dzanja lake lisachite chosalungama, woweruza zoona pakati pa munthu ndi mnzake,
9Ezk. 20.11amayenda m'malemba anga, nasunga maweruzo anga kuchita chokhulupirika; iye ndiye wolungama, adzakhala ndi moyo ndithu, anena Ambuye Yehova.
10Gen. 9.6Akabala mwana ndiye mkhungu, wokhetsa mwazi, wochita chimodzi cha izi,
11wosachita zabwino zonse zija, koma anadyanso pamapiri, naipsa mkazi wa mnansi wake,
12nasautsa osauka ndi osowa, natenga zofunkha, wosabwezera chigwiriro, nakweza maso ake kumafano, nachita chonyansa,
13Mac. 18.6napereka molira phindu, nalandira choonjezerapo; adzakhala ndi moyo uyu kodi? Sadzakhala ndi moyo, anachita zonyansa izi zonse; kufa adzafadi, mwazi wake umkhalira.
14Taona tsono, yemweyo akabala mwana uyu, naona zochimwa zonse adazichita atate wake, naopa wosachita zoterezo,
15wosadya pamapiri, kapena kukweza maso ake kumafano a nyumba ya Israele, wosaipsa mkazi wa mnansi wake,
16kapena kusautsa wina aliyense, wosatenga chigwiriro, wosatenga zofunkha; koma anapatsa wanjala chakudya chake, naveka wamaliseche ndi chovala,
17naletsa dzanja lake pa wozunzika, wosalandira phindu kapena choonjezerapo, wochita maweruzo anga, nayenda m'malemba anga; uyu sadzafera mphulupulu ya atate wake, adzakhala ndi moyo ndithu.
18Atate wake, popeza anazunza chizunzire, nafunkha za mbale wake, nachita chimene sichili chabwino pakati pa anthu ake, taona, adzafa mu mphulupulu yake.
19Eks. 20.5Koma inu mukuti, Alekeranji mwana kusenza mphulupulu za atate wake? Mwanayo akachita chiweruzo ndi chilungamo, nakasunga malemba anga onse, ndi kuwachita, adzakhala ndi moyo ndithu.
202Maf. 14.6; Yes. 3.10-11; Aro. 2.9; 6.23Moyo wochimwawo ndiwo udzafa; mwana sadzasenza mphulupulu za atate wake, ndi atate sadzasenza mphulupulu za mwana; chilungamo cha wolungama chidzamkhalira, ndi choipa cha woipa chidzamkhalira,
21Ezk. 33.12-19Koma woipayo akabwerera kusiya machimo ake onse adawachita nakasunga malemba anga onse, ndi kuchita chiweruzo ndi chilungamo, adzakhala ndi moyo ndithu, sadzafa.
22Nnena chimodzi chonse cha zolakwa zake zonse adazichita chidzakumbukika chimtsutse; m'chilungamo chake adachichita adakhala ndi moyo.
23Ezk. 33.11; 1Tim. 2.4Ngati ndikondwera nayo imfa ya woipa? Ati Ambuye Yehova, si ndiko kuti abwerere kuleka njira yake, ndi kukhala ndi moyo?
242Pet. 2.20Koma wolungamayo akabwerera kuleka chilungamo chake, nakachita mphulupulu, ndi kuchita monga mwa zonyansa zonse azichita woipa, adzakhala ndi moyo kodi? Nnena chimodzi cha zolungama zake zonse adzazichita chidzakumbukika m'kulakwa kwake analakwa nako, ndi m'kuchimwa kwake anachimwa nako; momwemo adzafa.
25Koma mukuti, Njira ya Ambuye njosayenera. Tamvera tsono nyumba ya Israele, Kodi njira yanga njosayenera? Njira zanu si ndizo zosayenera?
26Ezk. 18.24Wolungamayo akatembenukira kuleka chilungamo chake, nakachita mphulupulu, adzafa momwemo; m'mphulupulu yake adaichita adzafa.
27Ezk. 18.21Ndipo woipayo akatembenukira kuleka choipa chake adachichita, nakachita chiweruzo ndi chilungamo, adzapulumutsa moyo wake.
28Popeza anasamalira, natembenukira kuleka zolakwa zake zonse adazichita, adzakhala ndi moyo ndithu, sadzafa.
29Ezk. 18.25Koma nyumba ya Israele imanena, Njira ya Ambuye njosayenera. Inu, nyumba ya Israele, kodi njira zanga nzosayenera? Njira zanu si ndizo zosayenera?
30Mat. 3.2; Chiv. 2.5Chifukwa chake ndidzakuweruzani inu, nyumba ya Israele, yense monga mwa njira zake, ati Ambuye Yehova. Bwererani, nimutembenukire kuleka zolakwa zanu zonse, ndipo simudzakhumudwa nazo, ndi kuonongeka nayo mphulupulu.
31Aef. 4.22-24Tayani, ndi kudzichotsera zolakwa zanu zonse zimene munalakwa nazo, ndi kudzifunira mtima watsopano, ndi mzimu watsopano; pakuti mudzaferanji inu, nyumba ya Israele?
32Ezk. 18.23; 2Pet. 3.9Pakuti sindikondwera nayo imfa ya wakufayo, ati Ambuye Yehova; chifukwa chake bwererani, nimukhale ndi moyo.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.