1 2Ate. 2.3 Mkulu usamdzudzule, komatu umdandaulire ngati atate; anyamata ngati abale;
2akazi aakulu ngati amai; akazi aang'ono ngati alongo, m'kuyera mtima konse.
31Tim. 5.5, 16Chitira ulemu amasiye amene ali amasiye ndithu.
4Mat. 15.4Koma ngati wamasiye wina ali nao ana kapena adzukulu, ayambe aphunzire iwo kuchitira ulemu a m'banja lao, ndi kubwezera akuwabala; pakuti ichi ncholandirika pamaso pa Mulungu.
5Luk. 2.37Koma iye amene ali wamasiye ndithu, nasiyidwa yekha, ayembekezera Mulungu, nakhalabe m'mapembedzo ndi mapemphero usiku ndi usana.
6Koma iye wakutsata zomkondweretsa, adafa pokhala ali ndi moyo.
7Ndipo izi ulamulire, kuti akhale opanda chilema.
8Yes. 58.7Koma ngati wina sadzisungiratu mbumba yake ya iye yekha, makamaka iwo a m'banja lake, wakana chikhulupiriro iye, ndipo aipa koposa wosakhulupirira.
91Tim. 3.2Asawerengedwe wamasiye ngati sanafikire zaka makumi asanu ndi limodzi, atakhala mkazi wa mwamuna mmodzi,
10Luk. 7.38, 44; Mac. 16.15wa mbiri ya ntchito zabwino; ngati walera ana, ngati wachereza alendo, ngati adasambitsa mapazi a oyera mtima, ngati wathandiza osautsidwa, ngati anatsatadi ntchito zonse zabwino.
11Koma amasiye aang'ono uwakane; pakuti pamene ayamba kumchitira Khristu chipongwe afuna kukwatiwa;
12pokhala nacho chitsutso, popeza adataya chikhulupiriro chao choyamba.
132Ate. 3.11Ndipo aphunziraponso kuchita ulesi, aderuderu; koma osati ulesi wokha, komatunso alankhula zopanda pake, nachita mwina ndi mwina, olankhula zosayenera.
141Ako. 7.9; Tit. 2.8Chifukwa chake nditi akwatiwe amasiye aang'ono, nabale ana, naweruzire nyumba, osapatsa chifukwa kwa mdaniyo chakulalatira;
15pakuti adayamba ena kupatuka ndi kutsata Satana.
161Tim. 5.3, 5Ngati mkazi wina wokhulupirira ali nao amasiye, iye awathandize, ndipo Mpingowo usalemedwe; kuti uthandize iwo amene ali amasiye ndithu.
Ulamuliro wa aphunzitsi. Malangizo ena17 Afi. 2.29 Akulu akuweruza bwino ayesedwe oyenera ulemu wowirikiza, makamaka iwo akuchititsa m'mau ndi m'chiphunzitso.
18Deut. 25.4; Luk. 10.7Pakuti malembo ati, Usapunamiza ng'ombe yopuntha tirigu. Ndipo Wogwira ntchito ayenera kulipira kwake.
19Deut. 19.15Pa mkulu usalandire chomnenera, koma pakhale mboni ziwiri kapena zitatu.
20Iwo akuchimwa uwadzudzule pamaso pa onse, kuti otsalawo achite mantha.
211Tim. 6.13Ndikuchitira umboni pamaso pa Mulungu, ndi Khristu Yesu, ndi angelo osankhika, kuti usunge izi kopanda kusankhiratu, wosachita kanthu monga mwa tsankho.
22Mac. 6.6; 2Yoh. 11Usafulumira kuika manja pa munthu aliyense, kapena usayanjana nazo zoipa za eni; udzisunge wekha woyera mtima.
23Usakhalenso wakumwa madzi okha, komatu uchite naye vinyo pang'ono, chifukwa cha mimba yako ndi zofooka zako zobwera kawirikawiri.
24Agal. 5.19Zochimwa za anthu ena zili zooneka kale, zitsogola kunka kumlandu; koma enanso ziwatsata.
25Momwemonso pali ntchito zokoma zinaonekera kale; ndipo zina zosati zotere sizingathe kubisika.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.