1 Luk. 24.48; Mac. 1.8, 22; Aro. 8.17-18 Akulu tsono mwa inu ndiwadandaulira, ine mkulu mnzanu ndi mboni ya zowawa za Khristu, ndinenso wolawana nao ulemerero udzavumbulutsikawo:
2Yoh. 21.15-17; 1Ako. 9.17; 1Tim. 3.3, 8Wetani gulu la Mulungu lili mwa inu, ndi kuliyang'anira, osati mokakamiza, koma mwaufulu, kwa Mulungu; osatsata phindu lonyansa, koma mwachangu;
3Mat. 20.25-26; Afi. 3.17osati monga ochita ufumu pa iwo a udindo wanu, koma okhala zitsanzo za gululo.
41Ako. 9.25Ndipo pakuonekera Mbusa wamkulu, mudzalandira korona wa ulemerero, wosafota.
5Aro. 12.10; Yak. 4.6Momwemonso, anyamata inu, mverani akulu. Koma nonsenu muvale kudzichepetsa kuti mutumikirane; pakuti Mulungu akaniza odzikuza, koma apatsa chisomo kwa odzichepetsa.
6Yak. 4.10Potero dzichepetseni pansi padzanja la mphamvu la Mulungu, kuti panthawi yake akakukwezeni;
7Mat. 6.25ndi kutaya pa Iye nkhawa yanu yonse, pakuti Iye asamalira inu.
8Luk. 22.31Khalani odzisungira, dikirani; mdani wanu mdierekezi, monga mkango wobuma, ayendayenda ndi kufunafuna wina akamlikwire:
9Mac. 14.22; Yak. 4.7ameneyo mumkanize okhazikika m'chikhulupiriro, podziwa kuti zowawa zomwezo zilimkukwaniridwa pa abale anu ali m'dziko.
101Ako. 1.9; 2Ate. 2.17; Aheb. 13.21Ndipo Mulungu wa chisomo chonse, amene adakuitanani kulowa ulemerero wake wosatha mwa Khristu, mutamva zowawa kanthawi, adzafikitsa inu opanda chilema mwini wake, adzakhazikitsa, adzalimbikitsa inu.
111Pet. 4.11Kwa Iye kukhale mphamvu kunthawi za nthawi. Amen.
12 1Ako. 15.1; 2Ako. 1.19 Mwa Silivano, mbale wathu wokhulupirika monga ndimayesa, ndalembera kwa inu mwachidule, ndi kudandaulira, ndi kuchita umboni, kuti chisomo choona cha Mulungu ndi ichi; m'chimenechi muimemo.
13Mac. 12.12, 25Iye wa ku Babiloni wosankhidwa pamodzi nanu akukupatsani moni; ateronso Marko mwana wanga.
14Aro. 16.16; Aef. 6.23Mupatsane moni ndi kupsompsonana kwa chikondi.
Mtendere ukhale ndi inu nonse muli mwa Khristu.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.